Pitani ku nkhani yake

29 NOVEMBER, 2021
ANGOLA

“Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu” Latulutsidwa mu Chimbundu

“Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu” Latulutsidwa mu Chimbundu

Lamlungu pa 21 November 2021, M’bale Eric Raffaeli wa m’Komiti ya Nthambi ku Angola, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la pazipangizo za makono m’chilankhulo cha Chimbundu. Mabaibulo osindikizidwa adzayamba kupezeka mu 2022. Pulogalamu yochita kujambulidwayi inaulutsidwa pa intaneti ndipo anthu pafupifupi 11,000 anaonera pulogalamuyi.

Cha m’ma 1920, m’mayiko amene ankalamulidwa ndi dziko la Portugal analetsa kugwiritsa ntchito chilankhulo cha Chimbundu komanso zilankhulo zina za ku Africa kusukulu. Komabe, panopo anthu pafupifupi 1.7 miliyoni a ku Angola kuphatikizaponso ena omwe amakhala mu mzinda waukulu wa Luanda, amalankhula Chimbundu. Chilankhulochi ndi chimodzi mwa zilankhulo zikuluzikulu m’dzikoli.

Mabuku a Mboni za Yehova a m’Chimbundu anayamba kupezeka kuyambira cha m’ma 1990. Koma mpingo woyamba wa chilankhulochi unakhazikitsidwa mu 2008. Pofika pano pali mipingo yokwana 55 ya Chimbundu ndipo muli ofalitsa 2,614.

Mmodzi mwa amene amagwira nawo ntchito yomasulira mabuku m’Chimbundu akugwira ntchitoyi ali kunyumba

Baibuloli ndi losavuta kumva poyerekezera ndi Mabaibulo ena a m’chilankhulochi. Mwachitsanzo, lemba la Mateyu 5:3, m’Mabaibulo ena linamasuliridwa kuti: “Odala ndi anthu osauka muuzimu.” Koma Baibulo la Dziko Latsopano linamasulira lembali kuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira kuti amafunikira Mulungu.”

Mmodzi mwa amene anagwira nawo ntchito yomasulirayi ananena kuti: “Ndikukhulupirira kuti Baibuloli lithandiza kwambiri abale athu amene amalankhula Chimbundu. Liwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova akamaliphunzira paokha komanso akamaligwiritsa ntchito mu utumiki. Ndikuona kuti ndi mwayi kuti ndinagwira nawo ntchitoyi. Ndikuona kuti zikunditsimikizira kuti Mulungu ndi wokoma mtima kwambiri.”

Tikukhulupirira kuti Baibulo la m’Chimbunduli lithandiza kwambiri abale ndi alongo athu mu utumiki kuti apitirize kuthandiza anthu achidwi kuti ‘azizindikira zinsinsi zopatulika za ufumu wa Mulungu.’​—Luka 8:10.