Pitani ku nkhani yake

Tinasankha Kukhala Moyo Wosalira Zambiri

Tinasankha Kukhala Moyo Wosalira Zambiri

 Madián ndi mkazi wake Marcela ankakhala moyo wofewa mumzinda wa Medellín ku Colombia. Madián ankalandira ndalama zambiri ndipo ankakhala m’nyumba yokongola kwambiri. Komabe, monga atumiki a Yehova Mulungu, chinthu china chinawachititsa kuonanso bwino zinthu zimene ankaona kuti ndi zofunika kwambiri pa moyo wawo. Iwo anati: “Mu 2006, tinapita kumsonkhano wapadera wa tsiku limodzi wakuti ‘Khalanibe ndi Diso la Kumodzi.’ Nkhani zambiri pamsonkhanowu zinafotokoza kwambiri za kufunika kokhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti tiziwonjezera zimene timachita potumikira Mulungu. Pochoka kumsonkhanowo, tinazindikira kuti tikuchita zosemphana kwambiri ndi zimenezi. Tinkangokhalira kugula zinthu komanso tinali ndi ngongole yaikulu.”

 Atazindikira zimenezi, Madián ndi Marcela anayamba kusintha zinthu kuti akhale moyo wosalira zambiri. Iwo ananena kuti: “Tinachepetsa zinthu zomwe tinkagula. Tinasamukira m’nyumba yaing’ono, kugulitsa galimoto yathu ndipo tinagula njinga yamoto.” Iwo anasiyanso kupita kumashopu ndi cholinga choti asamakhale ndi mtima wongofuna kugula zinthu mwachisawawa. Anayamba kugwiritsa ntchito nthawi yawo yambiri pokambirana ndi anthu za Baibulo. Ndipo anayamba kumacheza ndi anzawo amene ankachita khama potumikira Yehova Mulungu. Mwachitsanzo anayamba kucheza kwambiri ndi apainiya apadera. *

 Pasanapite nthawi, Madián ndi Marcela anasankha zowonjezera utumiki wawo posamukira kumpingo wakumudzi kumene kunkafunika anthu ambiri olalikira. Kuti asamukire kumeneko, Madián anasiya ntchito yake. Bwana wake anaganiza kuti wachita wamisala moti n’chifukwa chake anaganiza zosiya ntchito. Koma Madián anamufunsa kuti: “Mumapeza ndalama zambiri, koma kodi ndinu wosangalala?” Iye anavomera kuti sasangalala chifukwa ali ndi mavuto ambiri omwe sangawathetse. Kenako Madián anamuuza kuti: “Choncho si ndalama zimene zimathandiza munthu kusangalala. Koma ndi zimene mumachita pa moyo. Ine ndi mkazi wanga timasangalala tikamaphunzitsa anthu za Mulungu ndipo tikufuna kuwonjezera nthawi imene timachita zimenezi n’cholinga choti tikhale osangalala kwambiri.”

 Madián ndi Marcela ndi osangalala kwambiri chifukwa choyesetsa kukwaniritsa zolinga zawo zauzimu. Pa zaka 13 zapitazi, akhala akutumikira m’mipingo imene ikufunikira olalikira ambiri kumpoto chakumadzulo kwa Columbia. Ndipo panopa ali ndi mwayi wotumikira monga apainiya apadera.

^ Apainiya apadera ndi anthu amene amaikidwa ndi ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova kuti azilalikira uthenga wabwino nthawi zonse m’madera ena. Iwo amalandira kangachepe kuti azipeza zofunika pa moyo.