Pitani ku nkhani yake

Anaphunzira kwa Akaidi

Anaphunzira kwa Akaidi

 Munthu wina wochokera ku Eritrea anathawa kwawo n’kupita ku Norway mu 2011. A Mboni za Yehova atakumana naye kuti amuuze uthenga wa m’Baibulo anawayankha kuti anakumanapo ndi a Mboni kwawo. Iye anafotokoza kuti pa nthawi imene anali msilikali ku Eritrea ankaona a Mboni omwe anali m’ndende akukana kukakamizidwa kulowa usilikali, ngakhale pamene ankawachitira nkhanza zoopsa.

 Zinazake zitachitika mwadzidzidzi, munthuyu anamangidwa n’kuikidwa m’ndende. Ndipo kundendeko anakakumana ndi a Mboni atatu, a Paulos Eyasu, a Negede Teklemariam, ndi a Isaac Mogos omwe anaikidwa m’ndende kuchokera m’chaka cha 1994 chifukwa cha chikhulupiriro chawo.

 Ali m’ndendemo, munthuyu anadzionera yekha kuti a Mboni amachita zimene amaphunzitsa ena pamoyo wawo. Ankaona kuti iwo amachita zinthu moona mtima komanso ankagawira akaidi ena zakudya zawo. Ankaonanso kuti akaidi omwe anali a Mboni ankaphunzira Baibulo limodzi tsiku lililonse komanso ankaitanira ena. Nthawi zinanso a Mboniwo ankapatsidwa mwayi woti atha kuwatulutsa m’ndende ngati atasainira kuti sakhalanso a Mboni, koma ankakana.

 Zimene munthuyu anaona zinamuchititsa chidwi ndipo atakhazikika ku Norway ankafuna kudziwa chifukwa chimene chimapangitsa a Mboni za Yehova kukhala ndi chikhulupiriro cholimba chonchi. Ndipo a Mboni atakumana naye, nthawi yomweyo anayamba kuphunzira Baibulo ndiponso kupita kumisonkhano yawo.

 Mu September 2018, anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Panopa amayesetsa kulalikira kwa anthu ochokera ku Eritrea ndi ku Sudan, n’kumawalimbikitsa kuti aziphunzira Baibulo kuti nawonso akhale ndi chikhulupiriro cholimba.