Pitani ku nkhani yake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Moyo Wanga Unkangoipiraipirabe

Moyo Wanga Unkangoipiraipirabe
  • Chaka Chobadwa: 1971

  • Dziko: Tonga

  • Poyamba: Ndinkagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, komanso ndinamangidwapo

KALE LANGA

 Banja lathu ndi la ku Tonga, ndipo lili ndi zilumba 170, kummwera chakumadzulo kwa nyanja ya Pacific. Ku Tonga tinalibe zinthu zambiri, tinkakhala nyumba yopanda magetsi komanso tinalibe galimoto. Koma tinali ndi madzi a pampopi, ndiponso tinali ndi nkhuku zochepa. Pa nthawi ya holide, ine ndi azichimwene anga awiri tinkapita kwa bambo kukawathandiza ntchito kufamu ya kwathu, yomwe tinkalimamo nthochi, zilazi, zakudya zina zotchedwa taro, ndi chinangwa. Kuwonjezera pa ndalama zochepa zomwe ankapeza akagwira maganyu, bambo ankagulitsanso mbewuzi kuti azikwanitsa kusamalira banja lathu. Mofanana ndi anthu ambiri okhala pazilumbazi, banja lathu linkalemekeza kwambiri Baibulo, ndipo nthawi zonse tinkapita kutchalitchi. Komabe, tinkaganiza kuti ngati titasamukira kudziko lina lolemera, tikhoza kukakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

 Ndili ndi zaka 16, ankolo anga anakonza zoti tisamukire ku California, m’dziko la U.S.A. Sizinali zophweka kuyamba moyo watsopano kumeneko. Zinthu zinayambadi kuyenda bwino pa nkhani ya ndalama, koma m’dera limene tinkakhalalo kunkachitika zachiwawa ndipo paliponse anthu ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Nthawi zambiri tinkamva kulira kwa mfuti usiku, ndipo maneba athu ambiri ankachita mantha ndi zigawenga. Anthu ambiri ankayenda ndi mfuti pofuna kudziteteza kapenanso pofuna kuthetsa mikangano. Mpaka pano ndili ndi chipolopolo pamtima chifukwa cha mikangano yomwe inachitika nthawi ina.

 Nditafika kusekondale, sindinkafuna kumaoneka otsalira kwa achinyamata anzanga. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuchita nawo maphwando aphokoso, kumwa mowa kwambiri, zachiwawa, komanso kugwiritsa ntchito mankhwala oletsedwa ndi boma. Ndinayambanso kukonda kwambiri mankhwala osokoneza bongo a cocaine. Koma kuti ndizipeza ndalama zogulira mankhwalawa, ndinayamba kuba. Achibale anga ankakonda kupita kutchalitchi, koma sankandipatsa malangizo aliwonse ondithandiza kuti ndizipewa kutengera anzanga omwe anali ndi makhalidwe oipa. Ndinkangokhalira kumangidwa chifukwa chochita zauchigawenga. Moyo wanga unkangoipiraipirabe. Pasanapite nthawi ananditsekeranso m’ndende.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

 Tsiku lina mu 1997, ndili kundende, mkaidi wina anandiona nditatenga Baibulo. Inali nthawi ya Khirisimasi, ndipo anthu a ku Tonga amaona kuti imeneyi ndi nthawi yapadera kwambiri. Mkaidiyo anandifunsa ngati ndikudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya kubadwa kwa Khristu, koma sindinkadziwa zomwe limanena. Ndiyeno anandiwerengera nkhani ya m’Baibulo yonena za kubadwa kwa Yesu. Atandifotokozera ndinazindikira kuti miyambo yambiri yomwe imachitika pa Khirisimasi sinatchulidwe n’komwe m’Baibulo. (Mateyu 2:1-12; Luka 2:5-14) Ndinadabwa kwambiri, ndipo ndinkaona kuti pali zinthu zinanso zoti ndiphunzire kuchokera m’Baibulo. Mlungu uliwonse munthuyo ankachita nawo misonkhano ya Mboni za Yehova yomwe inkachitikira kundendeko, ndiye ndinamupempha kuti tizipitira limodzi. Nthawi imeneyo ankakambirana za buku la m’Baibulo la Chivumbulutso. Zimene zinkafotokozedwa sindinkazimvetsa bwinobwino, koma chimene chinkandisangalatsa n’choti zomwe ankakambiranazo zinkachokera m’Baibulo.

 Ndinasangalala kwambiri a Mboniwo atandiuza kuti aziphunzira nane Baibulo. Kanali koyamba kuphunzira za lonjezo la m’Baibulo lakuti m’tsogolomu, padzikoli padzakhala paradaiso. (Yesaya 35: 5-8) Ndinazindikira kuti ndikufunikira kusintha zinthu pa moyo wanga kuti ndizisangalatsa Mulungu. Ndinadziwanso kuti Yehova Mulungu sangalole kuti ndidzalowe m’dziko latsopano ngati sindingasiye makhalidwe oipa. (1 Akorinto 6: 9, 10) Choncho ndinatsimikiza zosiya khalidwe langa losachedwa kupsa mtima, kusuta, kuledzera komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

 Mu 1999, ndisanamalize kugwira ntchito yanga ya ukaidi, akuluakulu a boma anandisamutsira kumalo ena osungira anthu amene analowa m’dzikolo popanda chilolezo. Kumeneko, chaka chinadutsa ndisanakumaneko ndi a Mboni. Komabe ndinali nditatsimikiza kuti ndipitirizabe kusintha makhalidwe anga. M’chaka cha 2000, boma la ku United States linakana pempho langa loti ndizikhalabe m’dzikolo, ndipo ananditumiza kwathu ku Tonga.

 Nditabwerera ku Tonga, ndinayesetsa kufunafuna kumene ndingapeze a a Mboni za Yehova ndipo ndinayambiranso kuphunzira Baibulo. Zimene ndinkaphunzira zinkandifika pamtima. Komanso ndinachita chidwi kwambiri nditaona kuti nawonso a Mboni a pachilumbachi ankagwiritsa ntchito Malemba pa chilichonse chomwe ankaphunzitsa, ngati mmenenso a Mboni a ku United States ankachitira.

 Bambo anga anali odziwika kwambiri kudera limene tinkakhala chifukwa choti anali ndi udindo waukulu kutchalitchi kwawo. Poyamba, anthu a m’banja langa anakhumudwa ataona kuti ndikugwirizana kwambiri ndi a Mboni za Yehova. Koma patapita nthawi, makolo anga anasangalala kwambiri ataona kuti mfundo zomwe ndinkaphunzira zikundithandiza kusintha makhalidwe anga oipa.

Mlungu uliwonse ndinkakonda kukamwa mowa wa kava ngati mmene amuna ambiri a ku Tonga amachitira

 Chimene chinandivuta kwambiri kuti ndisiye ndi mowa wotchedwa kava womwe anthu a chikhalidwe chathu amaukonda ndipo amaumwa mopitirira malire. Mlungu uliwonse amuna ambiri a ku Tonga amakonda kukamwa mowawu ndipo umapangidwa kuchokera ku mizu ya tsabola. Ndiye nditabwerera kwathu ku Tonga ndinayambanso zomwezo moti pafupifupi usiku uliwonse ndinkapita kumalo omwera kava ndipo ndinkaumwa mpaka kutsala pang’ono kukomoka nawo. Ndinkachita zimenezi chifukwa cha anzanga ocheza nawo omwe sankatsatira mfundo za m’Baibulo. Patapita nthawi, ndinathandizidwa kudziwa kuti Mulungu sakusangalala ndi zochita zanga. Ndiyeno ndinasintha n’cholinga choti Mulungu azindidalitsa komanso kuti azisangalala nane.

 Ndinayamba kupezeka pamisonkhano yonse ya Mboni za Yehova. Komanso kugwirizana ndi anthu omwe amakonda Mulungu kunandithandiza kuti ndizitha kupewa mayesero. Ndipo mu 2002, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

 Ndimasangalala chifukwa Mulungu wandilezera mtima monga mmene Baibulo limanenera kuti: “Yehova . . . akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Petulo 3:9) Akanatha kuwononga dziko loipali kalekale, koma walola kuti padutse nthawi yaitali kuti anthu ngati ine, tisinthe n’kukhala naye pa ubwenzi. Ndimaona kuti Yehova wandichitira zimenezi n’cholinga choti andigwiritsire ntchito kuti ndithandize anthu enanso kusintha.

 Yehova anandithandiza kusiya makhalidwe anga oipa omwe ankangoipiraipirabe. Panopa ndinasiya kubera anthu pofuna kupeza ndalama zokagulira mowa. Koma ndimayesetsa kuthandiza anthu ena kuti nawonso akhale paubwenzi wabwino ndi Yehova. M’gulu la Yehova, ndinapezamo mkazi dzina lake Tea, yemwe ndimamukonda kwambiri. Tili ndi mwana mmodzi wa mwamuna ndipo banja lathu limakhala mosangalala kwambiri. Tonse timaphunzitsa ena zomwe Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo kuti tidzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso komanso mwamtendere.