Pitani ku nkhani yake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Ndinkadzikumbira Ndekha Manda”

“Ndinkadzikumbira Ndekha Manda”
  • Chaka Chobadwa: 1978

  • Dziko: El Salvador

  • Poyamba: Ndinali M’gulu la Zigawenga

KALE LANGA

 Ndinadabwa munthu wina atandiuza kuti: “Ngati ukufuna kudziwa zoona zenizeni zokhudza Mulungu, usasiye kuphunzira Baibulo ndi a Mboni komanso kusonkhana nawo.” Pa nthawiyi ndinali nditayamba kuphunzira ndi a Mboni za Yehova. Koma kuti mumvetse chifukwa chake ndanena kuti zinandidabwitsa, ndiloleni ndikufotokozereni pang’ono mbiri yanga.

 Ndinabadwira m’tawuni ya Quezaltepeque, ku El Salvador. Ndine wa nambala 6 m’banja la ana 15. Makolo anga ankandiphunzitsa kuchita zinthu mwachilungamo komanso kumvera malamulo. Komanso wa Mboni wina dzina lake Leonardo ndi anzake ena, ankakonda kubwera kudzatiphunzitsa Baibulo. Koma zonse zomwe ndinkaphunzira ndinalibe nazo ntchito moti ndinkangokhalira kuchita zinthu zoipa. Ndili ndi zaka 14 ndinayamba kumwa mowa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi anzanga a kusukulu. Kenako mmodzi ndi mmodzi anayamba kusiya sukulu n’kukalowa gulu la zigawenga ndipo n’zomwe nanenso ndinachita. Tinkakonda kumangoyendayenda m’misewu n’kumabera anthu ndiponso kuwakakamiza kuti atipatse ndalama zomwe tinkalipirira mankhwala ozunguza bongo komanso zinthu zina zoipa.

 Ndinkaona kuti aliyense m’gulu la zigawengali ndi m’bale wanga ndipo ndinali wokonzeka kuchita chilichonse pofuna kumuthandiza. Mwachitsanzo, tsiku lina, mnzathu wina atasokonezeka kwambiri ndi mankhwala osokoneza bongo, anayamba kumenyana ndi neba wathu wina. Nebayo anagonjetsa mnzathuyo ndipo kenako anaimbira foni apolisi. Zimenezi zinandikwiyitsa kwambiri moti ndinayamba kuphwanya mawindo a galimoto ya nebayo ndi chibonga pofuna kuti amusiye mnzathuyo. Nebayo anayesetsa kundiletsa koma sindinamumvere moti galimotoyo inawonongeka kwambiri.

 Ndili ndi zaka 18, gulu lathu linamenyana ndi apolisi. Pamene ndinkafuna kuwaponyera bomba lokonza tokha, linandiphulikira m’manja. Sindikumbukira bwinobwino kuti linaphulika bwanji. Koma nditangoona kuti dzanja langa lanyenyeka, ndinakomoka. Pamene ndinkatsitsimuka kuchipatala, ndinazindikira kuti dzanja langa la kumanja laduka, khutu langa la kumanja lasiya kumva komanso diso langa la kumanja komweko, linali litasiya kuona bwinobwino.

 Ngakhale zinali choncho, nditangotuluka kuchipatalako, ndinapitanso ku gulu la zigawenga lija. Koma pasanapite nthawi apolisi anandimanga n’kukanditsekera kundende komwe kunalinso kale zigawenga zina. Kumeneko, ubwenzi wanga ndi zigawengazo unalimba kwambiri. Tsiku lililonse tinkachitira zinthu limodzi, kuyambira m’mawa pomwe tinkasutira limodzi chamba koyamba, mpaka nthawi yokagona.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

 Ndili m’ndende, Leonardo anabwera kudzandiona. Pamene tinkacheza, anandifunsa za tatuu imene inali pamkono wanga wakumanja, kuti: “Kodi ukudziwa kuti timadontho titatu iti tikuimira chiyani?” Ndinamuyankha kuti: “Ee, ndimadziwa. Timatanthauza chiwerewere, mankhwala osokoneza bongo komanso nyimbo zaphokoso.” Koma iyeyo ananena kuti: “Ine ndikuona kuti tanthauzo lake ndi chipatala, ndende komanso imfa. Pajatu unali m’chipatala, panopa uli m’ndende. Ndiye ukudziwa chimene chatsala?”

 Zimene Leonardo ananenazi zinandichititsa mantha chifukwa zinali zoona. Zimene ndinkachita zinali ngati ndikudzikumbira ndekha manda. Kenako anandipempha kuti aziphunzira nane Baibulo ndipo ndinavomera. Mfundo zimene ndinkaphunzira zinandithandiza kuti ndisinthe moyo wanga. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti “kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Choncho chinthu choyamba chomwe ndinkafunika kuchita chinali kusintha anthu ocheza nawo. Ndiyeno ndinasiya kupita kumisonkhano ya zigawenga, n’kuyamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova yomwe inkachitikira kundendeko. Kumisonkhanoko ndinakumana ndi mkaidi wina dzina lake Andrés, yemwe anabatizidwira kundende komweko n’kukhala wa Mboni za Yehova. Andrés anandipempha kuti tidyere limodzi chakudya cha m’mawa. Kungochokera nthawi imeneyo, m’malo moti tiziyamba tsiku ndi kusuta chamba, tinkayamba ndi kukambirana mfundo za m’Baibulo.

 Gulu la zigawenga lija linazindikira kuti ndayamba kusintha. Kenako mmodzi wa atsogoleri a zigawengazo anandiuza kuti akundifuna ndipo ndinachita mantha. Sindinkadziwa kuti andipanga zotani ndikamuuza kuti ndikufuna kusiya zauchigawenga, chifukwa sizikhala zophweka kutuluka m’gulu la zigawenga. Nditakumana naye, ananena kuti: “Taona kuti ukumapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova m’malo mobwera kumisonkhano yathu, maganizo ako ndi otani?” Ndinamuyankha kuti ndikufuna ndipitirize kuphunzira Baibulo kuti ndisinthe moyo wanga. Ndinadabwa akundiuza kuti gulu la zigawengalo lilola zimenezo pokhapokha ngati ndatsimizikadi kukhala wa Mboni za Yehova. Ndiyeno anapitiriza kuti: “Ngati ukufunadi kudziwa zoona zenizeni zokhudza Mulungu, usasiye kuphunzira ndi a Mboni za Yehova. Ifenso tikufuna kuti usiye kuchita zoipa. Wachita bwino kwambiri. Zimenezo nde nzeru, a Mboniwo akuthandiza. Inenso anandiphunzitsapo ndili ku United States moti anthu ena a kwathu ndi a Mboni. Pitiriza, usachite mantha.” Ndinkachitabe mantha koma pa nthawi imodzimodziyo ndinasangalala kwambiri. Nthawi yomweyo ndinathokoza Yehova Mulungu chamumtima. Ndinkangomva ngati mbalame yoti yamasulidwa pamsampha. Ndipo ndinamvetsa mawu a Yesu akuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:32.

 Koma nthawi zina anzanga ena omwe tinali limodzi m’gulu la zigawenga, ankandipatsa mankhwala osokoneza bongo pofuna kundiyesa. Ndivomereze kuti pena ndinkakanika kuugwira mtima moti ndinkalandira. Koma n’kupita kwa nthawi, komanso chifukwa chopemphera kwambiri kuchokera pansi pamtima, ndinakwanitsa kusiya makhalidwe anga oipa.​—Salimo 51:10, 11.

 Atanditulutsa m’ndende, anthu ambiri ankaganiza kuti ndikayambiranso kuchita zauchigawenga, koma ayi ndithu. Nthawi zambiri ndinkapitanso kundende komweko kukaphunzitsa akaidi zomwe ndinkaphunzira m’Baibulo. Pamapeto pake anzanga aja anakhulupirira kuti ndasinthadi. Komabe anthu omwe ndinkadana nawo pa nthawi imene ndinali chigawenga, sankadziwa kuti ndinasintha.

 Tsiku lina ndikulalikira limodzi ndi m’bale wina, ndinangozindikira kuti gulu la anthu lomwe linali ndi mfuti, landizungulira. Anthuwa anali a m’gulu linalake la zigawenga lomwe kale linkadana kwambiri ndi gulu lathu ndipo cholinga chawo chinali choti andiphe. M’bale amene ndinali naye uja anawafotokozera mwaulemu koma molimba mtima kuti ndinasiya kuchita zauchigawenga. Ndinayesetsa kuugwira mtima kuti ndisalimbane nawo. Atandimenya, anandichenjeza kuti ndisadzafikenso kudera limenelo, kenako anatsitsa mfuti zawo zija n’kutiuza kuti tizipita. Kunena zoona Baibulo linasinthadi moyo wanga. Likanakhala kale, ndikanamenyana nawo. Panopa ndimagwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo a pa 1 Atesalonika 5:15, akuti: “Onetsetsani kuti wina asabwezere choipa pa choipa kwa wina aliyense, koma nthawi zonse yesetsani kuchita zabwino kwa okhulupirira anzanu ndi kwa ena onse.”

 Kungoyambira pamene ndinakhala wa Mboni za Yehova, ndimayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo. Komabe kuchita zimenezi si kophweka ndipo ndimaona kuti Yehova Mulungu ndi amene amandithandiza. Mfundo za m’Baibulo komanso anzanga atsopano zimandithandizanso kwambiri. Sindilakalaka n’komwe kuyambiranso makhalidwe oipa omwe ndikachita kale.​—2 Petulo 2:22.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

 Poyamba ndinali wankhanza kwambiri komanso sindinkachedwa kupsa mtima. Ndimaona kuti ndikanapitiriza makhalidwe oipawa, bwenzi nditafa kalekale. Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinasintha moyo wanga moti panopa ndinasiya kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo komanso ndinaphunzira kukhala mwamtendere ndi anthu omwe poyamba anali adani anga. (Luka 6:27) Ndimasangalalanso kuti ndinapeza anzanga omwe amandithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. (Miyambo 13:20) Ndimamvanso bwino ndikaganizira kuti panopa moyo wanga uli ndi cholinga ndipo ndimatumikira Mulungu, yemwe ndi wokonzeka kundikhululukira zoipa zonse zomwe ndinkachita.​—Yesaya 1:18.

 Mu 2006, ndinaitanidwa kusukulu yapadera ya Akhristu osakwatira. Patadutsa zaka zingapo, ndinakwatirana ndi mkazi yemwe ndimamukonda kwambiri ndipo tonse tikuthandizana kulera mwana wathu wamkazi. Panopa, nthawi yanga yambiri ndimaigwiritsa ntchito pophunzitsa anthu mfundo za m’Baibulo zomwe zinandithandiza ineyo kusintha. Ndikutumikira monga mkulu mumpingo wathu ndipo ndimayesetsa kuthandiza achinyamata kuti asadzakumane ndi mavuto omwe ndinakumana nawo pa nthawi imene ndinali msinkhu wawowo. M’malo momadzikumbira manda anga omwe, ndikugwira ntchito yomanga tsogolo labwino n’kumayembekezera zimene Mulungu anatilonjeza kudzera m’Baibulo.