Pitani ku nkhani yake

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Britain—Gawo 6 (Kuyambira March Mpaka August 2018)

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Britain—Gawo 6 (Kuyambira March Mpaka August 2018)

Zithunzi izi zikusonyeza mmene ntchito yomanga ofesi ya nthambi yatsopano ya Mboni za Yehova inayendera ku Britain kuyambira mu March mpaka mu August 2018.

  1. Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana ya Kumpoto

  2. Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana ya Kum’mwera

  3. Maofesi

  4. Nyumba Yogona A

  5. Nyumba Yogona B

  6. Nyumba Yogona C

  7. Nyumba Yogona D

  8. Nyumba Yogona E

  9. Nyumba Yogona F

8 March, 2018—Malo a ofesi ya nthambi

M’modzi mwa anthu omwe amagwira ntchito yoonetsetsa kuti zachilengedwe zikusamaliridwa bwino, akuyeza madzi pa damu lomwe lili pafupi ndi khomo lolowera kuti aone ngati muli zinthu zimene zingathe kuwononga zamoyo.

13 March, 2018—Nyumba Yogona B

Mzimayi akuphunzira kuika mabolodi oteteza nyumba kuti isawonongeke chifukwa cha nyengo zosiyanasiyana. Mabolodi amenewa ali kunja kwa khoma la nyumba zogona lomwe mkati mwake muli njerwa komanso zinthu zooneka ngati thonje zomwe zimathandiza kuti m’nyumba musamazizire kwambiri.

5 April, 2018—Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana ya Kum’mwera

Thirakitala yosalazira msewu ikusalaza msewu asanathire phula. Mbali imeneyi ya msewu ili pafupi ndi Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana ya Kum’mwera ndipo ikamalizidwa zichititsa kuti msewu wozungulira malo onsewa ulumikizike.

1 May, 2018—Maofesi

Chithunzichi chinajambulidwa kuchokera m’mwamba kumpoto chakumadzulo kwa malowa. Mashini okwezera zinthu m’mwamba omwe akuoneka chakuno, ali pamene padzakhale malo olandirira alendo ku maofesi. Kumanja kwake kuli silabu ya pansi pa nyumba yomwe idzakhale maofesi pamene kumanzere kuli maziko a khitchini, chipinda chodyera ndi holo. Kanyumba komwe alendo amakwerapo kuti aone zinthu zakutali kasunthidwa n’kuikidwa pamalo oti azitha kuona bwinobwino mmene ntchito yomanga ikuyendera. Kanyumbaka ndi komwe kali kumanja pakona ya m’mwamba m’chithunzichi.

9 May, 2018—Maofesi

Zitsulo zomwe padzakhomedwe denga zikuikidwa m’malo ake, ndipo mbali imeneyi ndi komwe kudzakhale khitchini, malo odyera, holo, ndipo zonsezi zili m’nyumba yomwe mudzakhale maofesi.

14 May, 2018—Maofesi

M’modzi mwa anthu omwe amagwira ntchito yoonetsetsa kuti zachilengedwe zikusamaliridwa bwino akuyang’anira ntchito yokumba pofuna kuonetsetsa kuti mtengo womwe uli pamalowa sunaonongedwe. Okonza kaonekedwe ka malowa anaika zinthu zotchingira mtengowu kuzungulira mizu yake n’cholinga choti usaonongedwe. Mizu ya mitengo ina imatetezedwa ndi mpanda ndipo m’malo amenewa simuchitika ntchito yazomangamanga.

24 May, 2018—Nyumba Yogona E

Wokonza kaonekedwe ka malowa akuyala kapinga m’mbali mwa njira yodutsa anthu. Timitengo tomwe tikukhomedwato timathandiza kuti kapingayu asasunthe pamalo omwe waikidwa mizu yake ikamamera.

19 June, 2018—Nyumba Yogona D

Wopenta akulemba nambala pakhoma la matabwa yomwe ndi chizindikiro cha nsanjika yachitatu. M’mwezi wotsatira, ogwira ntchito yomanga anayamba kusamukira mu Nyumba Yogona D.

20 June, 2018—Maofesi

Makontilakita akuika masitepe opanga kale a konkire pamalo ake.

26 June, 2018—Maofesi

Ogwira ntchito yoika makoma opangidwa ndi mabolodi akuika maferemu a khoma la mukolido ku siling’i. Chakumanjaku kuli chipangizo chokwezera zinthu zolemera kwambiri m’mwamba ndipo amachigwiritsa ntchito poika mashini otenthetsera ndi oziziritsira mpweya.

10 July, 2018—Maofesi

Azimayi awiri akuika tizitsulo tomangira mapaipi pansi pomwe padzakhale malo olandirira alendo kumaofesi.

10 July, 2018—Nyumba Zogwirira Ntchito Zosiyanasiyana

Akuika ngalande ya madzi yomwe ili pakati pa Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana ya Kumpoto ndi Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana ya Kum’mwera.

17 July, 2018—Maofesi

Makontilakita akuika chigawo chomaliza cha kampanda ka padenga pamalo pake, panja pachipinda chodyeramo. Kutsogolo kwa khonde la zipilala lili m’munsimo kuli Nyumba Yogona A.

19 July, 2018—Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana ya Kum’mwera

Akuika zitsulo zadenga m’malo ake. Nyumbayi idzakhala malo ogwiriramo ntchito zamanja ndi maofesi.

2 August, 2018—Malo a ofesi ya nthambi

Chithunzichi chinajambulidwa kuchokera m’mwamba kumpoto chakumadzulo kwa malowa. Pakati kumanja, ntchito yoika zitsulo za Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana ya Kum’mwera yatha ndipo ntchito yoika khoma lakutsogolo kwa nyumbayi ili mkati. Chakutsogolo kuno, ntchito yomanga Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana ya Kumpoto ili mkati ndipo aika kale phula pa bwalo lomwe lili kutsogolo kwake. Pakati kumanzere kuli nyumba yomwe mudzakhale maofesi ndipo kutsogoloko kuli nyumba zogona.

3 August, 2018—Nyumba Zogona

Chithunzi chomwe chinajambulidwa kuchokera m’mwamba kum’mawa kwa malowa dzuwa likutuluka. Chakutsogolo kuno, Nyumba Zogona D, E, ndi F amaliza kumanga. Nyumba Yogona C akuyembekezera kudzamaliza mu October.

7 August, 2018—Maofesi

Akugwiritsa ntchito miyala ikuluikulu yozungulira pomanga khoma la damu. Malowa azidzakongoletsa pamalo olowera kumaofesi omwe akuoneka kumbuyo kwa mitengo.

7 August, 2018—Maofesi

Makalipentala akuika mashini otenthetsera ndi kuzizilitsira mpweya komanso mababu ku siling’i ya ofesi. Ofesiyi yakonzedwa n’cholinga chothandiza ogwira ntchito zosiyanasiyana kuyendetsa bwino ntchito zawo.

21 August, 2018—Maofesi

Akumanga ofesi pogwiritsa ntchito konkire yochita kuumba padera. Ntchitoyi inayenda mofulumira chifukwa chogwiritsa ntchito konkire yochita kuumbiratu moti pofika kumapeto kwa mwezi wa August anali atamaliza kumanga makoma onse a maofesi. Mawindo aakulu amathandiza kuti m’maofesi muziwala bwino chifukwa cha kuwala kochokera kunja. Mawindowa aikidwa mkati mwa khoma n’cholinga chochepetsa kuwala kwa dzuwa kwamphamvu komwe kumachitika m’nyengo yozizira komanso kutentha kwa dzuwa komwe kumabwera m’nyengo yotentha.

24 August, 2018—Maofesi

Akukonzekera kuika makoma okutira zitsulo za kudenga la chipinda chodyera ndi la holo. Makomawa azidzachepetsa phokoso pa nthawi yomwe malo awiriwa akuwagwiritsa ntchito nthawi imodzi.