Mboni za Yehova Padziko Lonse

Russia

NKHANI

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira ku Russia

Oimira gulu lina la zachitetezo la FSB anamanga a Dennis Christensen chifukwa chotenga nawo mbali pa msonkhano wa Mboni za Yehova womwe unkachitika mwamtendere mumzinda wa Oryol ku Russia.

NKHANI

Abale Anathandiza M’bale Konstantin Bazhenov Ali M’ndende, Atatulutsidwa Komanso Pomwe Ankatumizidwa Kwawo

M’bale Konstantin Bazhenov ndi mmodzi mwa a Mboni za Yehova omwe anamalizitsa zaka zake zokhala m’ndende kuchokera pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linaletsa ntchito yathu mu 2017. Atakhala m’ndende kwa chaka ndi miyezi 6, anatulutsidwa mofulumirirako pa 5 May 2021. Pambuyo pake anatumizidwa kwawo.

NKHANI

A Mboni za Yehova a ku Irkutsk Anakhalabe Okhulupirika Ngakhale Apolisi Anawachitira Nkhanza

Pa 4 October 2021, apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba zingapo m’chigawo cha Irkutsk. Anapanikiza anthu ndi mafunso komanso kuwamenya mwankhanza kwambiri. Pamapeto pake a Mboni za Yehova okwana 6, anakawatsekera m’ndende chifukwa chotsatira zomwe amakhulupirira.