Mboni za Yehova Padziko Lonse

Nepal

  • Mudzi wa Tharpu ku Nepal—Akukambirana mfundo za m’Baibulo ndi mlimi wolankhula Chitamang’i

Mfundo Zachidule—Nepal

  • 29,165,000—Chiwerengero cha anthu
  • 2,823—Chiwerengero cha Mboni za Yehova
  • 43—Mipingo
  • Pa anthu 10,465 alionse pali wa Mboni za Yehova m’modzi

GALAMUKANI!

“Chikondi Chimene Anatisonyeza Chinatikhudza Kwambiri”

Loweruka pa 25 April, 2015, ku Nepal kunachitika chivomerezi champhamvu kwambiri. Zimene a Mboni za Yehova anachita pambuyo pa chivomerezichi zinasonyeza kuti Akhristu enieni amakondana kwambiri.

NKHANI

A Mboni za Yehova Akuthandiza Anthu Okhudzidwa ndi Chivomerezi ku Nepal

A Mboni za Yehova ochokera ku mayiko 6 limodzi ndi komiti ya ku Nepal yopereka chithandizo pakagwa zamwadzidzidzi akuthandizabe anthu powapatsa zofunika pa moyo ndiponso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo.

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA)

Anadzipereka ndi Mtima Wonse

Alongo ambiri amene anasamukira kumayiko ena poyamba ankadzikayikira. Kodi anatani kuti alimbe mtima? Kodi aphunzirapo chiyani atatumikira kudziko lina?