Pitani ku nkhani yake

Kodi a Mboni za Yehova Ndi Gulu la Ziyoni?

Kodi a Mboni za Yehova Ndi Gulu la Ziyoni?

Ayi. A Mboni za Yehova ndi Akhristu ndipo zinthu zimene amakhulupirira zimachokera m’Malemba basi. Iwo samakhulupirira zimene zipembedzo zina zimakhulupirira zakuti kusonkhanitsidwa kwa Ayuda m’dziko la Palestine kukugwirizana ndi ulosi wa m’Malemba. Sakhulupirira zoti Malemba analosera kuti dziko la Palestine linasankhidwa mwapadera ndi Mulungu. Ndipotu Malemba sanena kuti dziko kapena mtundu winawake wa anthu ndi wapamwamba kuposa dziko kapena mtundu wina. Magazini ya Nsanja ya Olonda, yomwe imafalitsidwa ndi a Mboni za Yehova, inanena mosapita m’mbali kuti: “Malemba salimbikitsa gulu la ndale la Ziyoni.”

Buku lina limanena kuti gulu la Ayuda a Ziyoni ndi la ndale ndipo cholinga chawo ndi kulimbikitsa kuti dziko la Palestine likhale la chipembedzo chachiyuda. (Encyclopædia Britannica) Gulu la Ziyonili limaphatikiza zachipembedzo ndi zandale. Koma a Mboni za Yehova sakhulupirira kuti Ziyoni ndi mbali ya chiphunzitso cha chipembedzo, ndipo salowerera pa nkhani yokhudza ndale za Ziyoni.

Gulu la Mboni za Yehova ndi la chipembedzo ndipo sililowerera m’gulu lililonse la ndale, choncho sangakhale gulu la Ziyoni. Zoti a Mboni za Yehova sachita nawo ndale ndi zodziwika bwino moti m’mayiko ena a Mboni azunzidwapo chifukwa chosalowerera ndale. Timakhulupirira ndi mtima wonse kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha basi umene udzabweretse mtendere weniweni padziko lapansili osati boma kapena chipani chilichonse.

A Mboni za Yehova onse padziko lonse lapansi amayendera mfundo yakuti ayenera kumvera malamulo a dziko limene akukhala. Saukira boma kapena kumenya nawo nkhondo.