Pitani ku nkhani yake

Kodi a Mboni za Yehova Amaona Kuti N’kulakwa Kulandira Katemera?

Kodi a Mboni za Yehova Amaona Kuti N’kulakwa Kulandira Katemera?

 Ayi. A Mboni za Yehova saona kuti n’kulakwa kulandira katemera. Timaona kuti Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha ngati akufuna kulandira katemera kapena ayi. A Mboni za Yehova ambiri amasankha kulandira katemera.

 Timapita kuchipatala tikadwala ndipo timathokoza kwambiri kuti asayansi atulukira mankhwala othandiza pa matenda osiyanasiyana. Timathokozanso anthu ogwira ntchito kuchipatala omwe amadzipereka kwambiri, makamaka pa nthawi ya mavuto.

 A Mboni za Yehova amachita zinthu mogwirizana ndi akuluakulu oona za umoyo. Mwachitsanzo, kuyambira nthawi imene mliri wa COVID-19 unayamba, a Mboni za Yehova akhala akutulutsa nkhani m’zilankhulo mahandiredi ambiri pawebusaiti iyi kuti azikumbutsa anthu kuti azitsatira malangizo odzitetezera ku mliriwu. Malangizowa ndi okhudza kukhala motalikirana, kusasonkhana m’magulu, kukhala panyumba mukadwala, kusamba m’manja, kuvala chophimba kunkhope komanso zinthu zina zimene akuluakulu a boma akhala akulimbikitsa.—Aroma 13:1, 2.

 Kwa zaka zambiri, mabuku a Mboni za Yehova akhala akulimbikitsa mfundo zotsatirazi:

  •   Munthu ayenera kusankha yekha pa nkhani zokhudza mankhwala.—Agalatiya 6:5

     “[Magazini iyi] silimbikitsa anthu kuti alandire mankhwala aliwonse kuposa ena kapena chithandizo chakuchipatala chilichonse kuposa china ndipo sipereka malangizo okhudza mankhwala. Imangofotokoza mfundo zoona n’kumasiyira munthu amene wawerenga kuti asankhe yekha zochita.”—Galamukani! ya February 8, 1987.

     “Muyenera kusankha nokha ngati inu ndi ana anu alandire katemera kapena ayi.”—Galamukani! ya August 22, 1965.

  •   Timapita kuchipatala tikadwala chifukwa choti timaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali.—Machitidwe 17:28.

     “A Mboni za Yehova amapita kuchipatala komanso kumwa mankhwala akadwala. Iwo amakonda moyo ndipo amachita zonse zogwirizana ndi Malemba zimene angathe kuti ateteze moyo wawo.”—Nsanja ya Olonda ya July 1, 1975.

     “A Mboni za Yehova amamwa mankhwala akuchipatala ndiponso amalandira chithandizo chosiyanasiyana chimene achipatala amapereka. Iwo amafuna kukhala ndi thanzi labwino komanso moyo wautali. Ndipotu mofanana ndi Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi monga Luka, a Mboni za Yehova ena ndi madokotala. . . . A Mboni za Yehova amaona kuti ntchito imene madokotala komanso anthu ena azachipatala akugwira ndi yofunika kwambiri ndipo amayamikira khama limene anthu amenewa amasonyeza. Iwo amayamikiranso madokotala chifukwa cha mpumulo umene amapeza madokotalawo akawapatsa thandizo pa matenda awo.”—Nsanja ya Olonda ya February 1, 2011.