Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KHALANI MASO

N’chifukwa Chiyani Makhalidwe Abwino Alowa Pansi?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

N’chifukwa Chiyani Makhalidwe Abwino Alowa Pansi?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Masiku ano anthu ambiri sakusonyeza makhalidwe abwino. Odwala amwano amalalatira madokotala, mabwana a malesitanti amakalipira antchito awo, anthu opanda khalidwe akakwera mundege amanyoza ogwira ntchito mundegemo, ana a sukulu ovuta amanyoza, kuopseza komanso kuukira aphunzitsi ndipo andale ena amachita nawo zinthu zoipa pomwe ena amafuna kuonetsa kuti iwowo ali ndi abwino.

 Baibulo lili ndi malangizo odalirika otithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. Limafotokozanso chifukwa chake masiku ano anthu sakusonyeza makhalidwe abwino.

N’chifukwa Chiyani Makhalidwe Abwino Alowa Pansi?

 Zikuchita kuonekeratu kuti anthu ambiri padziko lonse lapansi sakusonyeza makhalidwe abwino.

  •   Malinga ndi kafukufuku waposachedwapa, anthu a ku America amakhulupirira kuti panopa makhalidwe a anthu alowa pansi kwambiri kuyerekeza ndi nthawi iliyonse pa zaka 22 zapitazi.

  •   Panali kafukufuku wina yemwe anachitika kwa anthu 32,000 a m’mayiko 28. Pakafukufukuyo, 65 peresenti ya anthuwo inanena kuti panopa anthu akuchita makhalidwe oipa kwambiri kuposa kale lonse.

 Baibulo linaneneratu kuti anthu azidzasonyeza makhalidwe omwe tikuwaona masiku ano.

  •   “Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, . . .  oopsa [ndiponso] osakonda zabwino.”​—2 Timoteyo 3:1-3.

 Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene ulosiwu ukukwaniritsidwira, werengani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?

Buku lothandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino

 Ngakhale kuti makhalidwe abwino m’dzikoli alowa pansi kwambiri, anthu mamiliyoni ambiri apeza kuti Baibulo ndi buku labwino kwambiri lothandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino. Malangizo ake “ndi odalirika nthawi zonse, kuyambira panopa mpaka kalekale.” (Salimo 111:8) Taganizirani zitsanzo zotsatirazi:

  •   Zimene Baibulo Limanena: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”​—Mateyu 7:12.

     Tanthauzo lake: Tizichitira anthu zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu ngati mmene ifeyo tingafunire kuti atichitire.

  •   Zimene Baibulo Limanena: “Popeza tsopano mwataya chinyengo, aliyense wa inu azilankhula zoona kwa mnzake, chifukwa ndife ziwalo zolumikizana.”​—Aefeso 4:25.

     Tanthauzo lake: Tizikhala oona mtima m’zolankhula ndi zochita zathu zonse.

 Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, werengani:

  •   Nsanja ya Olonda ya mutu wakuti “Kodi Tingapeze Kuti Malangizo Otithandiza Kusankha Zinthu Mwanzeru?

  •   Nkhani ya Chingelezi ya mutu wakuti “Tolerance​—How the Bible Can Help.”