Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yohane M’batizi Anakhalapodi?

Kodi Yohane M’batizi Anakhalapodi?

Nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zimatchula za munthu wina dzina lake Yohane M’batizi, yemwe ankalalikira za Ufumu wa Mulungu ku Yudeya. Kodi zimene Baibulo limanena za munthu ameneyu n’zoona? Taganizirani mfundo izi:

  • Baibulo limanena kuti: “Yohane M’batizi anapita m’chipululu cha Yudeya n’kuyamba kulalikira. Iye anali kulalikira kuti: ‘Lapani, pakuti ufumu wakumwamba wayandikira.’” (Mateyu 3:1, 2) Kodi zimene lembali limanena n’zogwirizana ndi zimene akatswiri olemba mbiri zakale anapeza? Inde.

    Katswiri wina wolemba mbiri yakale dzina lake Flavius Josephus anafotokoza za munthu wina dzina lake “Yohane M’batizi,” yemwe “ankalimbikitsa Ayuda kuti akhale olungama,” n’cholinga choti “adzipereke kwa Mulungu” komanso kuti “abatizidwe.”—Jewish Antiquities, Book XVIII.

  • Baibulo limanena kuti Yohane anadzudzula Herode Antipa, amene ankalamulira ku Galileya ndi ku Pereya. Herode anali Myuda yemwe ankaoneka kuti amatsatira Chilamulo. Yohane anadzudzula Herode chifukwa choti anakwatira Herodiya, mkazi wa m’bale wake. (Maliko 6:18) Akatswiri ena anafotokozaponso za nkhani imeneyi.

    Josephus, katswiri wolemba mbiri ananena kuti Antipa “anam’konda kwambiri Herodiya” ndipo “mopanda manyazi anamufunsira kuti amange naye banja.” Herodiya anavomera ndipo anasiya mwamuna wake n’kukwatirana ndi Antipa.

  • Baibulo limanenanso kuti “anthu ochokera ku Yerusalemu ndi ku Yudeya konse ndiponso ochokera m’midzi yonse yapafupi ndi Yorodano anali kubwera kwa iye [Yohane]. Iye anali kuwabatiza mumtsinje wa Yorodano.”—Mateyu 3:5, 6.

    Josephus anatsimikizira kuti zimenezi zinkachitikadi. Iye analemba kuti “khamu” la anthu linkabwera kudzaona Yohane ndipo “linkalimbikitsidwa komanso kukhudzidwa kwambiri ndi ulaliki wake.”

Apa n’zoonekeratu kuti Josephus, katswiri wolemba mbiri yakale, anatsimikizira mfundo yakuti Yohane M’batizi anakhalapodi. Ndipo ifenso tiyenera kukhulupirira zimenezi.