Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHINSINSI CHA BANJA LOSANGALALA

Zimene Banja la Ana Opeza Lingachite Kuti Lizigwirizana ndi Anthu Ena

Zimene Banja la Ana Opeza Lingachite Kuti Lizigwirizana ndi Anthu Ena

MARGARET, * MAYI AMENE AKULERA ANA OPEZA WA KU AUSTRALIA, ANANENA KUTI: “Mkazi woyamba wa mwamuna wanga ankauza ana ake kuti asamamvere chilichonse chimene ndingawauze. Anawauza kuti asamandimvere ngakhale pa zinthu zazing’ono ngati kuwauza kuti asaiwale kutsuka mkamwa.” Margaret amaona kuti banja lake silinkayenda bwino chifukwa cha zimene mkazi woyamba wa mwamuna wake ankauza anawo.

Mabanja amene ali ndi ana opeza amakumana ndi mavuto osiyanasiyana koma nthawi zambiri mavutowa amabwera chifukwa cha achibale kapena anzawo. * Makolo ambiri amene akulera ana opeza amafunika kugwirizana ndi mayi kapena bambo weniweni wa mwanayo pankhani zina monga nthawi yokamuona komanso chithandizo cha ndalama. Achibale komanso anthu ena angamavutikenso kuzolowerana ndi ana kapena kholo lopezalo. Mfundo za m’Baibulo zikhoza kuthandiza mabanja amene akulera ana opeza kulimbana ndi mavuto amene akukumana anawo.

VUTO LOYAMBA: KUSAGWIRIZANA NDI KHOLO LENILENI LA ANAWO

Mayi wina wa ku Namibia, dzina lake Judith, akulera ana opeza. Iye ananena kuti: “Mkazi woyamba wa mwamuna wanga anauza ana ake kuti ineyo ndangokhala mkazi wa bambo awo ndipo ngati titakhala ndi ana  sadzakhala abale awo. Mawu amenewa anandipweteka kwambiri chifukwa ineyo ndimawakonda kwambiri anawo ngati anga omwe.”

Akatswiri oona za m’banja amanena kuti banja likhoza kusokonekera ngati kholo lomwe likulera ana opeza siligwirizana ndi kholo lenileni la anawo. Nthawi zambiri amene sagwirizana ndi mayi amene akulera ana opezawo ndi mayi weniweni wa anawo. Ndiye n’chiyani chingathandize kuti azigwirizana?

Zimene mungachite kuti muzigwirizana: Muziika malire oyenerera. Ngati ndinu bambo kapena mayi weniweni wa anawo, muzilola kholo lawo kudzacheza nawo chifukwa mukapanda kutero, mwana wanu akhoza kukhala wosasangalala. * Tikutero chifukwa mwachibadwa, mwana amaona kholo limene ‘linamubereka’ kuti ndi lofunika kwambiri pa moyo wake. (Miyambo 23:22, 25) Komabe muzichita zimenezi mosamala. Zili choncho chifukwa ngati mulekerera kwambiri kholo linalo kuti likhale ndi mphamvu pakhomopo, mkazi kapena mwamuna wanu watsopanoyo akhoza kukhumudwa kwambiri. Choncho muziika malire kuti muteteze banja lanu. Mungamachite zinthu zina ndi mkazi kapena mwamuna wanu woyambayo koma muzichita mosamala.

ZIMENE MAKOLO ANGACHITE

  • Mukamalankhula ndi mkazi kapena mwamuna wanu woyamba, muzingokambirana zokhudza anawo osati nkhani zina. Mwachitsanzo, mungauze mkazi kapena mwamuna wanu woyambayo nthawi imene ayenera kuimba foni ngati akufuna kulankhula ndi anawo. Zimenezi zimathandiza kuti asamaimbe usiku kapena nthawi iliyonse imene angafune.

  • Ngati anawo akukhala ndi mwamuna kapena mkazi wanu woyamba, mwina zingakhale bwino kumacheza nawo pafoni, kuwalembera makalata kapena kuwatumizira mameseji. (Deuteronomo 6:6, 7) Zimenezi zingathandize kuti mudziwe zimene ana anu akufuna kapena mavuto amene akukumana nawo komanso zingathandize kuti muziwapatsa malangizo omwe angawathandize pamoyo wawo.

ZIMENE MAYI AMENE AKULERA ANA OPEZA ANGACHITE

  • Muzichita zinthu moganizira mayi weniweni wa anawo pomutsimikizira kuti simukufuna kumulanda ana akewo. (Afilipi 2:4; 1 Petulo 3:8) Muziuza mayiyo mmene anawo alili ndipo muzionetsetsa kuti mukuwauza zabwino zokhazokha. (Miyambo 16:24) Muziwapempha kuti akupatseni malangizo ena amene angakuthandizeni kuti muzilera bwino anawo ndipo muziwathokoza akakupatsani malangizowo.

  • Mayi awo akakhalapo muzipewa kuchita zinthu zosonyeza kuti mumawakonda kwambiri anawo. Beverly wa ku United States, yemwe akulera ana opeza, ananena kuti: “Mwana wanga wamng’ono wopeza ankafuna kumanditchula kuti Amami. Ndiye tinagwirizana kuti akhoza kumanditchula choncho tikakhala kunyumba koma pakakhala mayi ake kapena achibale a mayi ake asamanditchule choncho. Chifukwa cha zimenezi ineyo ndi mayi akewo timagwirizana moti nthawi zina timachitira zinthu limodzi pakakhala zochitika za kusukulu kwa mwanayo.”

Ana anu amasangalala mukamayesetsa kulankhulana nawo

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZIGWIRIZANA NDI MAKOLO A ANA ANU OPEZA

    Anthu amagwirizana akamapatsana ulemu

  • Mukakhala limodzi ndi anawo musamalankhule zoipa zokhudza makolo awo. N’zosavuta kuti muyambe  kulankhula zonyoza zomwe zingakhumudwitse kwambiri anawo. Nthawi ina anawo akhoza kudzauza kholo lawo zimene mumanenazo. (Mlaliki 10:20) Komanso ngati mwana atakuuzani kuti mayi ake enieni amakunenani, musakhumudwe kwambiri. M’malomwake, mungachite bwino kuganizira mmene zamukhudzira mwanayo. Mwina munganene kuti: “Usadandaule. Kungoti amayi ako akhumudwa ndipo nthawi zambiri anthu akakhumudwa amatha kulankhula zinthu zopsetsa mtima.”

  • Musamasinthesinthe malamulo amene munakhazikitsa komanso musamanyoze malamulo amene kholo linalo limapereka kwa ana akewo. Ngati malamulo amene mumauza anawo kuti azitsatira ali osiyana ndi a kholo linalo, afotokozereni anawo chifukwa chake. Mwachitsanzo, taonani mawu amene angakhale oyenera komanso osayenera:

    Mayi wolera ana opeza: Timoteyo, ukatsuke mbale yomwe wadyerayo.

    Timoteyo: Tikapita kwa amayi athu satitsukitsa mbale, timangozisiya amatsuka okha.

    Mayi wolera ana opeza (mokwiya): Ngati amakulekelerani ndi komweko, ine sindifuna ana aulesi!

    Kodi mawu amenewa ndi abwino?

    Mayi wolera ana opeza (modekha): Oo, kani? Koma kuno aliyense amatsuka yekha mbale imene wadyera.

  • Muzipewa kupatsa ana anu opezawo ntchito pa nthawi imene akufuna akacheze ndi kholo lawo lenileni. (Mateyu 7:12) Ngati mukuona kuti ntchitoyo ndi yofunika kuigwira mwansanga, pemphani kaye kholo lawo lenilenilo musanauze anawo kuti agwire ntchitoyo.

TAYESANI IZI: Mukadzakumananso ndi mwamuna kapena mkazi woyamba wa mkazi wanu kapena mwamuna wanu, mudzachite zotsatirazi:

  1. Mudzayesetse kukhala wansangala.

  2. Powapatsa moni mungachite bwino kugwiritsa ntchito dzina la mwana wawo amene mukulerayo. Mwachitsanzo, munganene kuti, “Mayi ake a Chifundo muli bwanji?”

  3. Mukakhala pa gulu muzipanga zinthu zoti kholo linalo lizilankhulapo.

VUTO LACHIWIRI: NGATI ANA OPEZA ALI AKULUAKULU

Buku lina lakuti Step Wars linanena kuti mayi wina, yemwe akulera ana opeza, ankadandaula kuti mwamuna wake amaikira kumbuyo ana ake aakuluakulu. Ndipo mwamunayo amawaikira ana akewo kumbuyo ngakhale anawo akamachitira mwano mayi awo opezawo. Mayiyo ananena kuti: “Zimenezi zimandikwiyitsa kwambiri.” Kodi mungatani kuti muteteze banja lanu ngati mukulera ana opeza omwe ndi akuluakulu?

Zimene mungachite kuti muzigwirizana: Muzichita zinthu mwachifundo. Baibulo limanena kuti: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:24) Muziyesetsa kuzindikira komanso kumvetsa zinthu zimene zikumudetsa nkhawa munthu winayo. Mwachitsanzo, ana opeza akakhala akuluakulu, amadera nkhawa kuti makolo awo enieni asiya kuwakonda kapena amaganiza kuti akamagwirizana kwambiri ndi kholo lopeza, ndiye kuti akunyoza kholo lawo lenilenilo. Pomwe kholo lenileni la anawo limada nkhawa kuti ngati saziwaikira kumbuyo, ana akewo akhoza kusiya kumukonda.

Musamakakamize ana anu opeza kuti azikukondani. Asiyeni kuti ayambe okha kukukondani. Si nzeru kukakamiza munthu wina kuti azikukondani. (Nyimbo ya Solomo 8:4) Choncho, musamayembekezere kuti mukangokwatirana, ana anu opeza ayamba kukukondani nthawi yomweyo.

Musamangonena chilichonse chimene chabwera m’maganizo mwanu. Muziganiza kaye musanalankhule ngakhale zitakhala kuti ana anu opeza sanakulankhuleni bwino. (Miyambo 29:11) Ngati mukuona kuti zikukuvutani kudzigwira, mungapemphere ngati mmene Mfumu Davide ya Isiraeli inachitira. Mfumuyo inapemphera  kuti: “Inu Yehova, ikani mlonda pakamwa panga. Ikani wolondera patsogolo pa milomo yanga.”—Salimo 141:3.

Ngati mukukhala m’nyumba imene anawo anakulira, mudzaona kuti pali zinthu zina za m’nyumbamo zimene amazikonda kwambiri. Pewani kusinthasintha zinthu makamaka m’zipinda zawo zogona. Mwina mungasankhe kusamuka n’kumakhala nyumba ina.

TAYESANI IZI: Ngati ana anu opeza akuluakulu akukuchitirani mwano kwambiri, muuzeni mkazi kapena mwamuna wanu kuti akuthandizeni. Musakakamize mwamuna kapena mkazi wanu kuti alange anawo. Yesetsani kuchita zinthu zimene zingathandize kuti inuyo ndi mwamuna wanuyo muzimvetsetsana. Mukakhala ndi “maganizo ogwirizana,” sizivuta kuthetsa mavuto.—2 Akorinto 13:11.

Muzisonyeza kuti mumakonda ana onse m’banja lanu latsopano

VUTO LACHITATU: ACHIBALE KOMANSO ANZANU

Marion, yemwe amakhala ku Canada ndipo akulera ana opeza, ananena kuti: “Nthawi zambiri makolo anga ankakonda kupatsa mphatso mwana wanga yekha kusiya ana a mwamuna wanga. Zikatero tinkatenga ndalama zathu n’kukawagulira nawonso mphatso, koma nthawi zina tinkalephera kuchita zimenezi chifukwa chosowa ndalama.”

Zimene mungachite kuti muzigwirizana: Muzikonda kwambiri banja lanu latsopanolo. Auzeni achibale anu komanso anzanu kuti muli ndi udindo wosamalira banja lanu latsopanolo. (1 Timoteyo 5:8) N’zoona kuti achibale anu komanso anzanu sangangoyamba lero ndi lero kukonda banja lanu latsopanolo, koma mungachite bwino kuwapempha kuti azilemekeza banja lanu. Afotokozereni kuti anawo akhoza kukhumudwa kwambiri ngati atamawachitira zinthu mwatsankho.

Muzionetsetsa kuti ana anu akucheza ndi agogo awo a mbali zonse. Mayi wina, dzina lake Susan wa ku England, ananena kuti: “Mwamuna wanga atamwalira ndinakwatiwanso patatha chaka ndi miyezi 6, koma apongozi anga sankagwirizana ndi mwamuna wanga watsopanoyo. Koma zinthu zinasintha titayamba kumawachezera, kumalola kuti zidzukulu zawo zizikacheza nawo komanso kuwayamikira pa zinthu zimene anatichitira.”

TAYESANI IZI: Ganizirani mnzanu kapena wachibale amene sagwirizana ndi banja lanu kenako mukambirane ndi mwamuna kapena mkazi wanu zimene mungachite kuti muyambirenso kugwirizana.

Mabanja amene ali ndi ana opeza amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Koma ngati banja lanu litamatsatira mfundo za m’Baibulo, likhoza kudzapeza madalitso amene Baibulo limafotokoza akuti: “Nzeru zimamanga banja la munthu, ndipo kuzindikira kumachititsa kuti lilimbe kwambiri.”—Miyambo 24:3.

^ ndime 3 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 4 Kuti mudziwe zambiri pankhaniyi, mungaone nkhani zoyambirira za m’magazini ya Galamukani! ya April 2012, yomwe ili ndi mutu wakuti, “Kodi Mabanja Amene Ali ndi Ana Opeza Angatani Kuti Zinthu Ziziwayendera?” yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 8 Ngati mwamuna kapena mkazi wanu woyamba amaopseza kapena kuchita zinthu zomwe zingasokoneze banja lanu, mungafunike kumukhwimitsira malamulo kuti muteteze banja lanu latsopanolo.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi ndingatani kuti ndizigwirizana ndi mkazi woyamba wa mwamuna wanga?

  • Kodi tingatani kuti achibale komanso anzathu asasokoneze banja lathu latsopano?