Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mu mzinda wa Nineve munali nyumba zochititsa chidwi komanso zipilala

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi n’chiyani chinachitikira mzinda wa Nineve pambuyo pa nthawi ya Yona?

CHA M’MA 670 B.C.E., ufumu wa Asuri unali wamphamvu kwambiri padziko lonse. Ndipo malinga ndi webusaiti ya malo osungirako zinthu zakale ya ku Britain, “ufumuwu unayambira kumadzulo ku Kupuro mpaka kukafika kum’mawa ku Iran ndipo pa nthawi ina unkalamuliranso ku Iguputo.” (The British Museum Blog) Likulu lake Nineve unali mzinda waukulu padziko lonse. Kunali minda ya maluwa yokongola, nyumba zachifumu zapamwamba komanso malaibulale akuluakulu. Zolemba pamakoma a mzinda wakale wa Nineve, zimasonyeza kuti Mfumu Ashabanipalu mofanana ndi mafumu ena a Asuri, ankadzitcha kuti “mfumu ya dziko lonse.” Pa nthawiyo Asuri komanso mzinda wawo wa Nineve ankaoneka kuti sangagonjetsedwe.

Ulamuliro wa Asuri unali ulamuliro wa mphamvu padziko lonse pa nthawiyo

Komabe Asuri atakhala amphamvu kwambiri, Yehova kudzera mwa mneneri Zefaniya ananeneratu kuti: “[Yehova] adzawononga Asuri. Adzachititsa Nineve kukhala bwinja, kukhala dziko lopanda madzi ngati chipululu.” Kuwonjezera pamenepo mneneri wa Yehova Nahumu ananeneratu kuti: “Funkhani siliva amuna inu, funkhani golide, . . . Mzindawu auchititsa kukhala wopanda kanthu ndipo ausandutsa bwinja. . . . Aliyense wokuona adzakuthawa ndipo adzanena kuti, ‘Nineve wasakazidwa!’” (Zef. 2:13; Nah. 2:9, 10; 3:7) Atamva maulosi amenewa n’kutheka kuti anthu ankakayikira kuti: ‘Koma zimenezi zingachitikedi? Kodi Asuri amphamvuwa angagonjetsedwedi?’ Ziyenera kuti zinali zovuta kukhulupirira.

Mzinda wa Nineve unakhala bwinja

Ngakhale zinali choncho panachitika zosayembekezereka. Chisanafike chaka cha 600 B.C.E., Ababulo ndi Amedi anaukira komanso kugonjetsa Asuri. Anthu anasiya kukhala ku Nineve ndipo n’kupita kwa nthawi anthu anaiwaliratu za mzindawu. Buku lina la kumalo ena osungirako zinthu zakale a ku New York linanena kuti, “pofika zaka za m’ma 500 mpaka 1500 anthu sankakhalanso mumzinda wa Nineve ndipo unakwiririka, moti anthu ankangomva za mzindawu akawerenga m’Baibulo.” Bungwe lina lofufuza zinthu zakale linanena kuti pofika zaka za m’ma 1800, “palibe ndi mmodzi yemwe amene ankadziwa ngati kunalidi likulu la Asuri lotchedwa Nineve.” (Biblical Archaeology Society Online Archive) Koma mu 1845 katswiri wa zinthu zakale dzina lake Austen Henry Layard anayamba kukumba pomwe panali mzinda wa Nineve. Zimene anapeza m’mabwinja amenewo zimasonyeza kuti mzinda wa Nineve unalidi wolemera kwambiri.

Kukwaniritsidwa kwa maulosi onena za mzinda wa Nineve, kumatitsimikizira kuti maulosi a m’Baibulo onena za kutha kwa maulamuliro andale, adzakwaniritsidwanso.​—Dan. 2:44; Chiv. 19:15, 19-21.