Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Lefèvre d’Étaples Ankafuna Kuti Anthu Wamba Adziwe Mawu a Mulungu

Lefèvre d’Étaples Ankafuna Kuti Anthu Wamba Adziwe Mawu a Mulungu

PA LAMLUNGU linalake chakumayambiriro kwa m’ma 1520, anthu okhala m’tauni ya Meaux, yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Paris, anadabwa kwambiri ndi zimene anamva kutchalitchi. Iwo anamva mabuku a Uthenga Wabwino akuwerengedwa m’chinenero chawo cha Chifulenchi m’malo mwa Chilatini ngati mmene zinkakhalira nthawi zonse.

Munthu amene anamasulira mabukuwo m’Chifulenchi, dzina lake Jacques Lefèvre d’Étaples, analembera mnzake wina kuti: “Ukhoza kudabwa ndi mmene Mulungu akuthandizira anthu m’madera ena kuti aphunzire Mawu ake.”

Pa nthawiyo, tchalitchi cha Katolika ndiponso akatswiri a maphunziro azachipembedzo a ku Paris ankaletsa anthu kuti aziwerenga Baibulo m’zinenero zimene anthu wamba ankalankhula. Ndiyeno n’chiyani chimene chinachititsa kuti Lefèvre amasulire Baibulo m’Chifulenchi? Nanga iye anathandiza bwanji anthu wamba kuti amvetse Mawu a Mulungu?

ANKAFUFUZA KUTI AMVETSE BWINO MALEMBA

Lefèvre anaona kuti m’mabuku akale a nzeru za anthu ndiponso azachipembedzo munali mfundo zina zolakwika chifukwa chomasuliridwa ndi anthu osiyanasiyana pamene zaka zinkadutsa. Asanayambe ntchito yomasulira Baibulo, iye ankagwira mwakhama ntchito yokonza mfundo zolakwika m’mabukuwo. Pofufuza tanthauzo lenileni la mabuku akalewa, anayamba kuphunzira kwambiri Baibulo limene Akatolika ankagwiritsa ntchito la Latin Vulgate.

Atayamba kuphunzira Malemba mwakhama, anaona kuti “kuphunzira mfundo zochokera kwa Mulungu n’kumene kungathandize munthu . . . kukhala wosangalala kwambiri.” Choncho Lefèvre anasiya kuphunzira mabuku a nzeru za anthu ndipo anaika mtima wake wonse pa kumasulira Baibulo.

Mu 1509, Lefèvre anatulutsa buku lokhala ndi mabuku 5 a Masalimo * omasuliridwa m’Chilatini. Limodzi mwa mabukuwa linali lomwe iye analimasulira n’cholinga choti akonze zolakwika za m’Baibulo la Latin Vulgate. Mosiyana ndi akatswiri ena a Baibulo pa nthawiyo, Lefèvre anayesetsa kumasulira Malemba m’njira yosavuta kumva. Izi zinathandiza kwambiri akatswiri ena a Baibulo ndiponso anthu amene ankafuna kusintha zikhulupiriro zachikatolika.—Onani bokosi lakuti, “ Kodi Zimene Lefèvre Anachita Zinathandiza Bwanji Martin Luther?”

Tchati cha mayina audindo a Mulungu a m’buku la Masalimo chimene chimapezeka m’buku la Lefèvre limene linasindikizidwa mu 1513

Lefèvre anali Mkatolika ndipo ankakhulupirira kuti tchalitchichi chikhoza kusintha pokhapokha anthu wamba ataphunzitsidwa Malemba molondola. Koma kodi anthuwo akanamvetsa bwanji Malemba popeza Mabaibulo ambiri ankangopezeka m’Chilatini?

ANTHU ANAYAMBA KUPEZA BAIBULO MOSAVUTA

Mawu amene Lefèvre analemba kumayambiriro kwa Baibulo lake la mabuku a Uthenga Wabwino amasonyeza kuti ankafunitsitsa kuti Baibulo lizipezeka mosavuta kwa anthu onse m’zinenero zawo

Lefèvre ankakonda kwambiri Mawu a Mulungu moti anayesetsa kuti Baibulo lizipezeka mosavuta kwa anthu ambiri. Kuti izi zitheke, mu June 1523 anatulutsa Baibulo laling’ono la mabuku a Uthenga Wabwino m’Chifulenchi. Popeza Baibuloli linali laling’ono kwambiri, linali lotsika mtengo kwambiri poyerekezera ndi Mabaibulo ena ndipo anthu osauka ankatha kuligula.

Atangotulutsa Baibuloli, anthu ambiri analigula. Anthuwa anali ofunitsitsa kwambiri kuwerenga uthenga wa Yesu m’chinenero chawo moti Mabaibulo okwana 1,200 amene anasindikizidwa anatha patangodutsa miyezi yochepa.

ANATSUTSA ATSOGOLERI ACHIPEMBEDZO MOLIMBA MTIMA

M’mawu oyamba a Baibuloli, Lefèvre anafotokoza kuti anamasulira mabuku a Uthenga Wabwino m’Chifulenchi n’cholinga choti “anthu wamba azidziwa bwino mfundo zoona za m’Baibulo mofanana ndi anthu amene ankawerenga Baibulo m’Chilatini.” Koma kodi n’chifukwa chiyani Lefèvre ankafunitsitsa kuti anthu wamba azimvetsa bwino Baibulo?

Iye ankadziwa kuti tchalitchi cha Katolika chinali chitasokonezedwa ndi zikhulupiriro komanso nzeru za anthu. (Maliko 7:7; Akolose 2:8) Choncho ankaona kuti nthawi inali itakwana yoti Uthenga Wabwino “ulengezedwe molondola kwa anthu padziko lonse n’cholinga choti asapitirize kusocheretsedwa ndi zikhulupiriro za anthu.”

Lefèvre anayesetsa kuulula kuti anthu amene ankaletsa kumasulira Baibulo m’Chifulenchi analibe zifukwa zomveka. Iye anawadzudzula chifukwa cha chinyengo chawo ponena kuti: “Kodi angaphunzitse bwanji [anthu] kuti azisunga zonse zimene Yesu Khristu anawalamula ngati sakufuna kuti anthuwo aziwerenga Uthenga wa Mulungu m’chinenero chawo?”—Aroma 10:14.

Chifukwa cha zimenezi, akatswiri a maphunziro azachipembedzo pa yunivesite ya Paris anayesa kuletsa Lefèvre kuti asaulule chinyengo chawo. Mu August 1523, akatswiriwa anayesanso kuletsa ntchito yofalitsa Mabaibulo ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo amene anamasuliridwa m’zinenero za anthu wamba. Anachita zimenezi poganiza kuti zikhoza “kusokoneza zinthu m’tchalitchi cha Katolika.” Mfumu Francis I ya ku France ikanapanda kulowererapo, Lefèvre akanaweruzidwa kuti ndi wampatuko.

ANAMALIZA KUMASULIRA BAIBULO MOBISA

Lefèvre sankalola kuti anthu otsutsawo azimusokoneza pa ntchito yake yomasulira Baibulo. Iye atamaliza kumasulira Malemba Achigiriki, kapena kuti Chipangano Chatsopano, mu 1524 anatulutsa buku la Masalimo limene anamasulira m’Chifulenchi. Anachita zimenezi chifukwa chofuna kuthandiza anthu kuti azipemphera “ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso mochokera pansi pa mtima.”

Akatswiri a maphunziro azachipembedzo pa yunivesite ya Paris anawerenga Baibulo la Lefèvre ndiponso zinthu zina zimene analemba n’cholinga choti aone ngati munali mfundo zolakwika. Atawerenga analamula kuti Baibulo lake la Malemba Achigiriki liwotchedwe anthu akuona komanso anaweruza kuti zinthu zina zimene Lefèvre analemba “zinkalimbikitsa anthu kutsatira Luther, yemwe anali wampatuko.” Akatswiriwa atamuitana kuti akafotokoze maganizo ake, Lefèvre anasankha kuti asanene chilichonse ndipo anathawira ku Strasbourg. Atafika kumeneko, anapitiriza kumasulira Baibulo mobisa. Ngakhale kuti ena anaona kuti Lefèvre wachita mantha, iye ankaona kuti ndi njira yabwino imene akanayankhira anthu omwe sankayamikira n’komwe mfundo zamtengo wapatali za m’Baibulo.—Mateyu 7:6.

Patadutsa chaka pafupifupi chimodzi Lefèvre atathawira ku Strasbourg, Mfumu Francis I inamusankha kuti aziphunzitsa mwana wake wazaka 4, dzina lake Charles. Zimenezi zinamuthandiza kuti akhale ndi nthawi yokwanira yomasulira Baibulo lonse. Mu 1530, anamaliza Baibuloli ndipo analisindikiza kunja kwa dziko la France. Mfumu Charles V inavomereza kuti lisindikizidwe mumzinda wa Antwerp. *

ZINA ZIMENE ANKAYEMBEKEZERA SIZINACHITIKE

Pa moyo wake wonse, Lefèvre ankafuna kuti tchalitchi cha Katolika chisiye kutsatira miyambo ya anthu n’kuyamba kuphunzitsa mfundo zoona za m’Baibulo. Iye ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti “Mkhristu aliyense ali ndi ufulu komanso udindo wowerenga ndiponso kuphunzira Baibulo payekha.” N’chifukwa chake anayesetsa kuthandiza kuti Baibulo lizipezeka mosavuta kwa anthu onse. Lefèvre anagwira ntchito yotamandika ngakhale kuti zimene ankafuna kuti tchalitchi cha Katolika chichite sizinatheke. Iye anathandiza kwambiri kuti anthu wamba adziwe bwino Mawu a Mulungu.

^ ndime 8 M’bukuli munali madanga 5 ndipo buku lililonse la Masalimo linali m’danga lakelake. Bukuli linalinso ndi tchati cha mayina audindo a Mulungu ndiponso zilembo 4 zachiheberi zoimira dzina lenileni la Mulungu.

^ ndime 21 Patapita zaka 5 mu 1535, womasulira wina wachifulenchi dzina lake Olivétan anatulutsa Baibulo lake lomasuliridwa kuchokera ku zinenero zoyambirira za Baibulo. Pomasulira Malemba Achigiriki anadalira kwambiri zimene Lefèvre analemba.