Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Timaphunzira za Mulungu Kuchokera kwa Aneneri Ake

Timaphunzira za Mulungu Kuchokera kwa Aneneri Ake

Kale, Mulungu ankauza aneneri ake mauthenga ofunikira okhudza anthu. Kodi mauthengawa angatithandize kudziwa zimene tiyenera kuchita kuti Mulungu azitidalitsa? Inde. Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa aneneri okhulupirika atatu.

ABULAHAMU

Mulungu alibe tsankho ndipo akufuna kuti anthu onse alandire madalitso.

Mulungu analonjeza mneneri Abulahamu kuti: “Mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso chifukwa cha iwe.”​—Genesis 12:3.

Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Mulungu amatikonda kwambiri ndipo akufuna kuti mabanja onse alandire madalitso, kutanthauza amuna, akazi ndi ana amene amamumvera.

MOSE

Mulungu ndi wachifundo ndipo amadalitsa anthu amene amachita khama kuti amudziwe.

Mulungu Wamphamvuyonse anapatsa mneneri Mose mphamvu zochitira zozizwitsa zikuluzikulu. Komabe, Mose anapemphera kuti: “Ndidziwitseni njira zanu, kuti ndikudziweni, kutinso mundikomere mtima.” (Ekisodo 33:13) Mulungu anasangalala ndi zimene Mose anapempha ndipo anamudalitsa pomuwonjezera luso lodziwa ndi kumvetsa njira zake ndiponso makhalidwe ake. Mwachitsanzo, Mose anaphunzira kuti Mlengi ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo.”​—Ekisodo 34:6, 7.

Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Mulungu akufuna kudalitsa tonsefe kaya ndife amuna, akazi kapena ana ngati tikufunitsitsa kumudziwa bwino. M’Malemba Opatulika, iye amasonyeza mmene tiyenera kumulambirira komanso kuti ndi wofunitsitsa kutichitira chifundo ndi kutidalitsa.

YESU

Mwachifundo, Yesu anachiritsa matenda a mitundu yonse

Tingasangalale ndi madalitso osatha ochokera kwa Mulungu tikamaphunzira zokhudza Yesu, zimene anachita ndi zimene anaphunzitsa.

Tikamawerenga Mawu a Mulungu, tingaphunzire zambiri zokhudza moyo wa Yesu ndi zimene ankaphunzitsa. Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zochitira zozizwitsa zambiri monga kuchiritsa anthu olumala, a vuto losaona komanso a vuto losamva. Yesu anaukitsanso akufa. Zimene Yesu anachitazi ndi umboni wakuti m’tsogolomu Mulungu adzadalitsa anthu onse. Iye anafotokoza zimene wina aliyense angachite kuti adzalandire madalitso amenewa. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”​—Yohane 17:3.

Yesu anali wachifundo ndiponso wokoma mtima. Amuna ndi akazi, ana komanso okalamba anapita kwa iye atawapempha mwachikondi kuti: “Phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mateyu 11:29) Mosiyana ndi anthu ena a m’nthawi yake amene ankachitira nkhanza azimayi, Yesu ankawachitira zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu.

Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Yesu anasonyeza kuti amakonda anthu ndipo anatisiyira chitsanzo cha mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi ena.

YESU SI MULUNGU

Malemba Opatulika amatiphunzitsa kuti “kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi” ndipo Yesu Khristu anali mneneri wodzichepetsa wa Mulungu. (1 Akorinto 8:6) Yesu ananena momveka bwino kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa iyeyo ndiponso kuti Mulungu ndi amene anamutuma padziko lapansi.​—Yohane 11:41, 42; 14:28. *

^ ndime 17 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Yesu Khristu, onani phunziro 4 m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera Kwa Mulungu komwe kakupezekanso pa intaneti pa www.pr418.com/ny.