Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | BAIBULO—BUKU LOMWE LINAPULUMUKA M’ZAMBIRI

Baibulo Linasungidwa Ngakhale Kuti Ena Ankalitsutsa

Baibulo Linasungidwa Ngakhale Kuti Ena Ankalitsutsa

VUTO LIMENE LINALIPO: Atsogoleri ambiri andale komanso azipembedzo sankafuna kuti anthu adziwe uthenga wa m’Baibulo. Choncho iwo ankagwiritsa ntchito udindo wawo poletsa anthu kumasulira, kusindikiza ngakhalenso kukhala ndi Baibulo. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri:

  • Cha m’ma 167 B.C.E.: Mfumu Antiyokasi Epifanasi yemwe ankafuna kukakamiza Ayuda kuti azitsatira chipembedzo chachigiriki, analamula kuti Malemba onse Achiheberi awonongedwe. Wolemba mbiri wina dzina lake Heinrich Graetz, ananena kuti nduna za mfumuyi “zikapeza mipukutu ya Chilamulo, zinkaing’amba ndiponso kuitentha nthawi yomweyo. Komanso zinkapha aliyense amene wapezeka akuwerenga Baibulo pofuna kulimbikitsidwa ndiponso kutonthozedwa.”

  • Zaka za m’ma 500 mpaka 1500: Atsogoleri ena achikatolika ankakhumudwa chifukwa choti anthu a m’chipembedzochi ankalimbikitsa ena kutsatira mfundo za m’Baibulo m’malo mwa zikhulupiriro zachikatolika. Iwo ankafuna kuti anthu aziwerenga buku la Masalimo la m’Chilatini basi. Ndipo anthu wamba omwe anali ndi mabuku ena a m’Baibulo, ankawanena kuti ndi ampatuko. Pamsonkhano wina wa tchalitchichi anasankha anthu oti “azifufuza mwakhama anthu ampatuko . . . m’nyumba ndiponso m’zipinda zonse zapansi, zomwe ankazikayikira kuti akusungirako mabuku a m’Baibulo. . . . Ndipo nyumba iliyonse yomwe apezako wampatuko, aziigwetsa.”

Anthuwa akanakwanitsadi kuwononga Baibulo, ndiye kuti uthenga wake ukanatheranso pomwepo.

Baibulo lachingelezi lomasuliridwa ndi William Tyndale, linapulumuka ngakhale kuti pa nthawiyi Mabaibulo ena analetsedwa komanso kuwotchedwa. William anaphedwa mu 1536.

ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE: Ngakhale kuti Mfumu Antiyokasi inkafuna kuti Baibulo lisapezekenso ku Isiraeli, Ayuda ambiri anali atasamukira m’mayiko osiyanasiyana. Ndipotu akatswiri amanena kuti pomwe inkafika nthawi ya Yesu, n’kuti Ayuda oposa 60 pa 100 alionse akukhala m’madera a kunja kwa dziko la Isiraeli. Ayudawa ankasunga mipukutu ya Malemba m’masunagoge awo ndipo ndi yomwenso anthu ena kuphatikizapo Akhristu, ankaigwiritsa ntchito.Machitidwe 15:21.

M’zaka za m’ma 500 mpaka 1500, anthu ena analimba mtima n’kulolera kuzunzidwa ndipo anapitiriza kumasulira ndi kukopera Baibulo pamanja. Zikuoneka kuti pofika cha m’ma 1400, mabuku ena a m’Baibulo ankapezeka m’zinenero pafupifupi 33, ngakhale kuti pa nthawiyi kunalibe makina osindikizira mabuku. Patapita nthawi, anthu anayamba kumasulira komanso kusindikiza Mabaibulo m’zinenero zinanso zambiri.

ZOTSATIRA ZAKE: M’nkhaniyi taona kuti atsogoleri ena andale komanso azipembedzo ankafuna kuwononga Baibulo, koma sizinatheke. Baibulo lamasuliridwa komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse. Lathandizanso mayiko ambiri pa nkhani zokhudza malamulo ndi zinenero. Komanso lathandiza anthu ambiri kusiya makhalidwe oipa.