Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Nyenje za Moyo Wautali

Nyenje za Moyo Wautali

NYENJE zimafananirako ndi ziwala ndipo zimapezeka pafupifupi m’zigawo zonse za dziko lapansi kupatulako ku Antarctica. Koma kumpoto chakummawa kwa dziko la America kumapezeka nyenje zochititsa chidwi kwambiri zomwe zimakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali.

Taganizirani izi: Nyenje za mtunduwu zimayamba kupezeka zambirimbiri m’nyengo yozizira, koma kwa milungu yochepa. Pa nthawiyi zimafundula, zimaimba kwambiri, zimaulukauluka, zimaikira mazira kenako zimafa. Koma chochititsa chidwi n’chakuti mazirawo akaswa, ana amadzaonekera pambuyo pa zaka 13 kapena 17, potengera mtundu wake. Ndiyeno n’chiyani chimachitikira anawa pa nthawi yonseyi?

Kuti tipeze yankho la funsoli tiyeni tione moyo wa nyenjezi. Pakadutsa mlungu umodzi kuchokera pamene nyenje za mtunduwu zatuluka pansi, zazimuna ndi zazikazi zimakumana, kenako zazikazi zimaikira mazira 400 mpaka 600 pakhungwa la mtengo. Zikatere, nyenje zazikuluzo zimafa. Mazirawa amaswa pakadutsa milungu ingapo ndipo tiana timagwera pansi n’kulowa m’dothi. Pansipo timayamwa madzi a m’mizu ya mitengo kwa zaka zambiri n’kumapitiriza kukula. Kenako pambuyo pa zaka 13 kapena 17 zimakhala zitakula ndipo zimatuluka pansipo. Pambuyo pa mlungu umodzi nazonso zimaikira mazira kenako zimafa.

Magazini ina inafotokoza kuti: “Kwa zaka zambiri, asayansi akhala akuyesetsa kuti amvetse mmene moyo wa nyenjezi umayendera koma alephera. . . . Ndipo ngakhale masiku ano akatswiri a tizilombo akuyesetsa kuti amvetse mmene moyo wa tizilomboti unayambira.” (Nature) Nawonso ofufuza za moyo wa zinyama amagoma ndi mmene nyenjezi zimakulira.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zomwe taona zokhudza moyo wa nyenjezi, zikugwirizana ndi mfundo yakuti zamoyo zimachita kusintha kuchokera ku zinthu zina? Kapena zikusonyeza kuti zinachita kulengedwa?