Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kudana ndi Kusagwirizana ndi Zakudya kwa Thupi N’kosiyana Bwanji?

Kodi Kudana ndi Kusagwirizana ndi Zakudya kwa Thupi N’kosiyana Bwanji?

Mtsikana wina dzina lake Emily anati: “Ndinayamba kumva zosakhala bwino ndipo ndinangoika foloko m’mbale. Ndinangoona kuti mkamwa mukuyabwa komanso lilime layamba kutupa. Ndinayamba chizungulire ndiponso kubanika, kenako zidzolo zinayamba kutuluka m’manja ndi m’khosi momwe. Ndinayesetsa kunyalanyaza zomwe zinkandichitikirazo komabe ndinaona kuti ndikufunika kupita kuchipatala mwamsanga.”

ANTHU ambiri angavomereze kuti kudya n’kosangalatsa. Komabe pali anthu ena amene thupi lawo limadana ndi zakudya zinazake ngati mmene zilili ndi Emily. Ndipo vuto la Emily ndi lalikulu kwambiri. Koma n’zosangalatsa kuti mavuto ambiri a kudana ndi zakudya sakhala oopsa.

M’zaka zaposachedwapa, anthu ambiri akumapezeka ndi mavuto odana ndi zakudya zinazake. Komabe zotsatira za kafukufuku wina zikusonyeza kuti ngakhale kuti anthu ambiri amanena kuti ali ndi vutoli, ndi ochepa chabe amene amapezekadi nalo akayezedwa.

Kodi Chimachitika N’chiyani Kuti Thupi Lizidana Ndi Zakudya Zina?

Lipoti lina linanena kuti: “Chimene chimachititsa kuti thupi lizidana ndi zakudya zinazake sichidziwika bwinobwino.” Lipotili linalembedwa m’magazini ina ndi gulu la asayansi lomwe mtsogoleri wawo ndi Dr.  Jennifer J. Schneider Chafen. (The Journal of the American Medical Association) Komano akatswiri ambiri amakhulupilira kuti nthawi zambiri vutoli limayambika chifukwa cha chitetezo cha m’thupi.

Nthawi zina vutoli limayamba chifukwa chakuti chakudya chimene munthu wadya chili ndi pulotini winawake. Ndiyeno chitetezo cha m’thupi chimaona ngati pulotini ameneyu ndi poizoni. Kenako pulotiniyu akalowa m’thupi, chitetezo cha m’thupi chimapanga asilikali enaake pofuna kuteteza thupi. Ndiyeno munthu akadzadyanso chakudyacho asilikali aja amatulutsa madzi osungunula pulotini yemwe thupi likumuwona ngati poizoni wa m’chakudyacho.

Komatu zimenezi pazokha sikuti zili ndi vuto lililonse. Komabe pa zifukwa zosadziwika bwino, zikuoneka kuti kupangidwa kwa asilikaliwa komanso kuchuluka kwa madzi osungunula poizoni n’komwe kumayambitsa zizindikiro zosonyeza kuti munthu akudana ndi chakudya chinachake.

N’chifukwa chake anthu ena amati akadya chakudya chinachake koyamba sakhala ndi vuto lina lililonse, koma akadzachidyanso thupi lawo limasonyeza zizindikiro zoti likudana nacho.

N’chiyani Chimachitika Kuti Thupi Lisamagwirizane ndi Zakudya Zinazake?

Pali zizindikiro zosiyanasiyana zimene munthu amene sagwirizana ndi zakudya zinazake angasonyeze mofanana ndi munthu yemwe ali ndi vuto lodana ndi zakudya. Mosiyana ndi vuto lodana ndi zakudya, vuto la kusagwirizana ndi zakudya limayambika chifukwa chakuti chakudya sichikugayika. Nthawi zambiri thupi la munthu amene ali ndi vutoli limalephera kugaya zakudya mwina chifukwa chakuti timadzi tomwe timagaya zakudya n’tochepa. Mwinanso chingakhale chifukwa chakuti tinthu tina tomwe tili m’chakudyacho n’tovuta kugayika. Mwachitsanzo, anthu ena sagwirizana ndi mkaka chifukwa choti thupi lawo limalephera kutulutsa timadzi togaya mtundu winawake wa shuga yemwe amapezeka mumkakamo.

Popeza kuti vutoli silokhudzana ndi chitetezo cha m’thupi, munthu amayamba kuvutika akangodya chakudya koyamba. Nthawi zina munthu akadya chakudya chochepa amakhala bwinobwino, koma akadya chambiri m’pamene amavutika. Zimenezitu n’zosiyana ndi vuto la kudana ndi zakudya chifukwa munthu yemwe thupi lake limadana ndi zakudya akhoza kudwala ngakhale atangodya kachakudya kochepa.

Kodi Zizindikiro za Mavutowa N’zotani?

Ngati muli ndi vuto lodana ndi zakudya zinazake mungasonyeze zizindikiro zotsatirazi: Kutupa kukhosi, maso kapenanso lilime; kuyabwa, zidzolo, mseru, kusanza, kutsekula m’mimba, ndipo zikafika povuta mungachite chizungulire, kukomoka, mtima umapopa magazi pang’onopang’ono mwinanso ungasiye kugunda. Kwa anthu amene ali ndi vuto lalikulu ngati Emily tamutchula uja, zizindikirozi zingaonjezeke mofulumira kwambiri ndipo moyo wawo ungakhale pangozi.

Thupi la munthu likhoza kudana ndi chakudya chamtundu uliwonse. Komabe ndi zakudya zochepa zomwe zimayambitsa mavuto akuluakulu. Zakudyazi ndi monga: mkaka, mazira, nsomba, nkhanu, mtedza, soya komanso tirigu. Ndipotu munthu aliyense akhoza kukhala ndi vutoli posatengera msinkhu wake. Kafukufuku akusonyeza kuti ana akhoza kutengera vutoli kuchokera kwa makolo awo. Komabe zikuoneka kuti nthawi zambiri ana akakula amasiya kudana ndi zakudyazi.

Zizindikiro za vuto losagwirizana ndi zakudya zinazake si zodetsa nkhawa kwenikweni poyerekezera ndi za vuto lodana ndi zakudya. Zizindikiro za vuto losagwirizana ndi zakudya zinazake ndi monga kupweteka m’mimba, kufufuma mimba, kukungika kwa minofu, kuwawa kwa mutu, nsungu kapenanso kumva kutopa. Kawirikawiri vutoli limayamba pambuyo podya zakudya za m’gulu la mkaka, tirigu, mowa komanso zokhala ndi yisiti.

Mmene Mungadziwire Mavutowa ndi Mmene Mungawachepetsere

Ngati mukuona kuti muli ndi vuto lodana kapena kusagwirizana ndi zakudya, mungachite bwino kupita kuchipatala kuti mukayezedwe. Kungoganiza kuti muli ndi vuto n’kuthamangira kusiya zakudya zinazake sikungakuthandizeni chifukwa zikhoza kuchititsa kuti thupi lanu lizisowa zinthu zina zofunikira kwambiri.

Njira yabwino kwambiri yochepetsera mavutowa n’kupeweratu zakudya zomwe zimayambitsa mavutowo. * Koma ngati vuto lanu silalikulu, mungachite bwino kumadya zakudya zochepa kapenanso kumazidya pakapita nthawi. Anthu ena amakakamizika kupeweratu zakudya zomwe amadana nazo kapenanso kumadya mwa apa ndi apo potengera kukula kwa vuto lawo.

Choncho ngati muli ndi vuto la kudana kapena kusagwirizana ndi zakudya zinazake, dziwani kuti anthu ambiri omwenso ali ndi mavutowa anaphunzira zomwe angachite kuti achepetse vuto lawolo ndipo akusangalalabe ndi zakudya zina zabwino komanso zopatsa thanzi.

^ ndime 19 M’madera ena madokotala amalimbikitsa anthu amene ali ndi vuto lodana ndi zakudya zinazake kuti aziyenda ndi mankhwala enaake oti azitha kudzibaya mwamsanga vutoli likayambika. M’madera enanso madokotala amanena kuti ana amene ali ndi vutoli angachite bwino kuvala chibangiri kapena chizindikiro china chomwe chingathandize aphunzitsi awo kudziwa kuti ali ndi vutoli.