Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Anandithandiza pa Nthawi Yomwe Ndinkafunikiradi Kuthandizidwa

Yehova Anandithandiza pa Nthawi Yomwe Ndinkafunikiradi Kuthandizidwa

Zimene zinandichitikira tsiku lina m’chaka cha 1991, zinasinthiratu moyo wanga. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 20.

NDINABADWIRA mumzinda wa Szerencs ndipo ndinakulira m’mudzi wotchedwa Tiszaladány womwe uli kumpoto, chakum’mawa kwa dziko la Hungary. Tsiku lina mu June 1991, ine ndi anzanga tinapita pamalo enaake omwe sitinkawadziwa bwino kuti tikasambire. Malowa ali mu mtsinje wa Tisza. Titangofika pamalowa, ndinadumphira m’madzi poganiza kuti ndi akuya. Koma ndikanadziwa sindikanachita zimenezi. Nkhope yanga inagunda pansi ndipo ndinathyoka khosi komanso ndinavulala mtsempha wotumiza mauthenga ku ubongo. Ndinayesetsa kuti ndidzuke koma ndinalephera kusuntha manja ndi miyendo yanga. Ndinayesanso kudzutsa mutu kuti ndizipuma bwino, koma zinakanika ndipo ndinayamba kumwa madzi. Mnzanga wina ataona kuti sindikutha kusuntha, anabwera n’kundivuula.

Ngakhale kuti sindinakomoke, ndinali nditavulala koopsa. Munthu wina anaimba foni kuchipatala ndipo kunabwera ndege kudzanditenga. Madokotala anayesetsa kundithandiza kuti ndikhalenso bwino. Kenako, anandisamutsira kumalo ena othandizira anthu olumala omwe ali mumzinda wa Budapest, likulu la dzikoli. Kwa miyezi itatu sindinkatha kukhala tsonga ndipo ndinkangogona chagada. Ndinkangokwanitsa kusuntha mutu, koma kuchokera m’mapewa kupita mmunsi, ziwalo zonse zinali zitafa. Zimenezi zinachititsa kuti ndizidalira ena kuti andichitire chilichonse. Izi zinkandikhumudwitsa kwambiri moti ndinkangolakalaka nditafa.

Nditatulutsidwa m’chipatala, makolo anga anaphunzitsidwa zimene azichita pondisamalira. Koma ntchito yondisamalira inali yotopetsa komanso inkapangitsa kuti azikhala ndi nkhawa. Patatha chaka, nanenso ndinayamba kudwala matenda ovutika maganizo. Zimenezi zinapangitsa kuti andipezere akatswiri odziwa za matendawa omwe anandipatsa malangizo osiyanasiyana. Izi zinandithandiza kuti ndisamadandaule kwambiri ndi vuto langa la kulumala.

Ndinayambanso kuganizira kwambiri zokhudza moyo. Ndinkadzifunsa kuti, kodi cholinga cha Mulungu chinali chiyani polenga anthufe? N’chifukwa chiyani ndinakumana ndi vuto limeneli? Ndinawerenga mabuku ndi magazini osiyanasiyana kuti ndipeze mayankho, koma sizinathandize. Kenako ndinayamba kuwerenga Baibulo, koma sindinkalimvetsa, choncho ndinasiya kuliwerenga. Kuwonjezera pamenepa, ndinafunsa wansembe wina kuti andithandize koma sanandiyankhe zogwira mtima.

Kenako m’chaka cha 1994, kunyumba kwathu kunabwera a Mboni za Yehova awiri ndipo bambo anawauza kuti akambirane ndi ineyo. Iwo anandifotokozera kuti Mulungu walonjeza kuti adzakonza dzikoli n’kukhala paradaiso. Anandiuzanso kuti adzathetsa matenda komanso mavuto onse. Izi zinandisangalatsa kwambiri koma ndinkakayikira ngati zinali zoona. Komabe ndinalandira mabuku awo awiri othandiza kuphunzira Baibulo ndipo ndinawawerenga. A Mboniwa atabweranso anandipempha kuti aziphunzira nane Baibulo ndipo ndinavomera. Anandilimbikitsanso kuti ndizipemphera kwa Mulungu.

Ndinayamba kuona kuti Mulungu amandikonda

A Mboniwa ankagwiritsa ntchito Baibulo kuyankha mafunso anga onse. Kenako ndinayamba kuona kuti Mulungu amandikonda. Nditaphunzira Baibulo kwa zaka ziwiri, pa September 13, 1997 ndinabatizidwa kunyumba kwathu m’bafa. Tsiku limeneli ndi losaiwalika pa moyo wanga.

Mu 2007, anandipititsanso mumzinda wa Budapest, kumalo osamalira anthu olumala aja. Mpaka pano ndikukhalabe komweku. Zimenezi zathandiza kuti ndikhale ndi mwayi wouza anthu zinthu zosangalatsa zomwe ndaphunzira m’Baibulo. Nyengo ikakhala kuti ili bwino, ndimatuluka panja n’kumakauza anthu uthenga wa m’Baibulo. Zimenezi zimatheka chifukwa ndili ndi njinga ya olumala imene anaipanga mwapadera. Ndimayendetsa njingayi pogwiritsa ntchito chibwano.

Banja lina la mumpingo wathu linandipatsa ndalama ndipo ndinagula laputopu. Laputopuyi ndimaigwiritsa ntchito poimba foni kudzera pa Intaneti komanso kulemba makalata kwa anthu amene sapezeka panyumba anthu a mumpingo mwathu akamalalikira. Koma popeza manja anga sagwira ntchito, ndimachita zonsezi posuntha mutu wanga. Kuchita zimenezi kwandithandiza kuti ndizolowere kulankhula ndi anthu komanso kuti ndisamangoganiza za mavuto anga.

Ndimauza anthu uthenga wa m’Baibulo kudzera pa Intaneti

Ndimakwanitsanso kusonkhana limodzi ndi anthu a mumpingo mwathu. Ndikafika ku Nyumba ya Ufumu, a Mboni anzanga amandinyamula pa masitepe ndikamalowa komanso ndikamatuluka. Ikafika nthawi yoti anthu ayankhe, munthu amene wakhala nane pafupi amaimika mkono m’malo mwa ineyo. Kenako amandinyamulira Baibulo kapena buku limene tikuphunzira, ineyo n’kumayankha.

Nthawi zonse ndimamva ululu ndipo sinditha kupanga zinthu pandekha. Nthawi zina ndimakhumudwa chifukwa cha zimenezi. Koma ndimalimba mtima ndikaganizira za ubwenzi wanga ndi Yehova Mulungu, chifukwa ndimadziwa kuti ndikamamuuza zakukhosi kwanga m’pemphero, amandimvetsera. Komanso ndimalimbikitsidwa kuchokera pa zimene ndimawerenga m’Baibulo tsiku lililonse. Ndimalimbikitsidwanso ndi zimene a Mboni anzanga amandichitira, kuphatikizapo kundipempherera. Zimenezi zimandithandiza kuti ndisamangoganizira za mavuto anga.

Ndimaona kuti Yehova anandithandiza kwambiri ndipo anachita zimenezi pa nthawi yomwe ndinkafunikiradi kuthandizidwa. Komanso wandilonjeza kudzera m’Mawu ake kuti ndidzakhala ndi thanzi labwino m’dziko latsopano. Choncho ndimayembekezera nthawiyi, pomwe ndizidzatha ‘kuyenda, kudumphadumpha ndi kutamanda Mulungu’ chifukwa cha chikondi ndi kukoma mtima kwake.—Machitidwe 3:6-9.