Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Chiseyeye

Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Chiseyeye

CHISEYEYE ndi amodzi mwa matenda ofala kwambiri padziko lonse. Matendawa akamayamba kumene, zizindikiro zake sizimaonekera msanga. Chifukwa chakuti anthu sadziwa mwachangu kuti akudwala chiseyeye, matendawa amabweretsa mavuto aakulu. Magazini ina inanena kuti chiseyeye chili m’gulu la matenda a m’kamwa amene “amayambitsa mavuto aakulu pa moyo wa anthu ambiri.” Magaziniyi inanenanso kuti matendawa amachititsa “munthu kumva kupweteka, kuvutika kudya komanso kulephera kuseka ndi kulankhula momasuka.” (International Dental Journal) Tiyeni tikambirane zina ndi zina zokhudza matendawa zomwe zingatithandize kuti tiwapewe.

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Matendawa

Matenda a chiseyeye ali ndi masiteji osiyanasiyana. Siteji yoyamba ndi kutupa kwa nkhama. Pa sitejiyi, nkhama zimatuluka magazi. Izi zimatha kuchitika munthu akamatsuka m’kamwa komanso akamayeretsa mano pogwiritsa ntchito kaulusi. Nthawi zinanso magazi amangotuluka okha. Komanso munthu amatha kutuluka magazi m’nkhama adokotala akamafufuza kuti aone ngati nkhama zake zili ndi vuto.

Pa siteji yachiwiri, nkhama komanso mafupa amene amathandiza kuti mano akhale olimba amayamba kuwonongeka. Matendawa akafika siteji imeneyi sasonyeza zizindikiro nthawi yomweyo, koma amayamba kuonetsa zizindikiro pakapita nthawi. Zizindikiro zake ndi monga, kununkha m’kamwa, kugwedera mano, kutuluka magazi m’nkhama, pamakhala mpata pakati pa mano kapena pakati pa nkhama ndi mano komanso nkhama zimachoka, zimene zimapangitsa kuti mano azioneka aatali.

Zimene Zimayambitsa Matendawa Komanso Kuipa Kwake

Pali zinthu zambiri zimene zingapangitse kuti munthu adwale chiseyeye. Nthawi zambiri matendawa amayamba ndi mabakiteriya amene amakhala m’mano. Mabakiteriyawa akapanda kuchotsedwa, amapangitsa kuti nkhama ziyambe kutupa. Nkhama zikapitiriza kutupa, zimayamba kulekana ndi  mano ndipo zimenezi zimapangitsa kuti mabakiteriyawo alowe m’kati mwa nkhamazo n’kuyamba kuchulukana. Mabakiteriyawa akachuluka, amayamba kuwononga mafupa komanso nkhama. Ndiponso amayambitsa zinthu zachikasu zomwe zimakhala zovuta kuchotsa chifukwa zimakakamira kwambiri ku mano. M’zinthu zachikasu zimenezi mumakhalanso mabakiteriya omwe amapitiriza kuwononga nkhama.

Palinso zinthu zina zimene zingapangitse kuti munthu adwale chiseyeye. Zina mwa zinthuzi ndi kusatsuka m’kamwa, kumwa mankhwala amene angapangitse kuti chitetezo cha m’thupi chitsike, matenda oyambitsidwa ndi mavairasi, kusintha kwa mahomoni kumene kumachitika mzimayi akakhala ndi pakati, nkhawa, matenda a shuga, kumwa mowa kwambiri komanso kusuta fodya.

Matenda a chiseyeye amabweretsanso mavuto ena pa moyo wa munthu. Mwachitsanzo, mano akamapweteka kapena akachoka, zimapangitsa kuti munthu azilephera kutafuna chakudya komanso kuchimva kukoma. Munthu amavutikanso kulankhula komanso saoneka bwino. Ndiponso akatswiri ofufuza zaumoyo anapeza kuti kusatsuka m’kamwa kumayambitsa matenda ambiri a m’kamwa.

Zizindikiro za Chiseyeye Komanso Mmene Matendawa Angachizidwire

Kodi mungadziwe bwanji kuti mwayamba kudwala chiseyeye? Kodi mwayamba kuona zizindikiro zofanana ndi zimene tazifotokoza m’nkhaniyi? Ngati zili choncho, mungachite bwino kukaonana ndi dokotala wodziwa bwino za mano.

Kodi n’zotheka kuchiza matendawa? N’zotheka ngati angoyamba kumene. Koma ngati matendawa afika poipa, pamangofunika kupeza njira yothandiza kuti asapitirize kuwononga mafupa komanso nkhama. Madokotala a mano amakhala ndi zipangizo zimene zimawathandiza kuchotsa zinthu zachikasu zimene zimakakamira m’mano.

Anthu ena sangakwanitse kuonana ndi dokotala amene angawathandize komanso sangathe kulipira ndalama zofunika atadwala matendawa. Ndiyetu njira yabwino kwambiri ndi kupewa. Kuti mupewe matendawa muyenera kumatsuka m’kamwa nthawi zonse.