Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mbalame Yotha Kuuluka Ulendo Wautali

Mbalame Yotha Kuuluka Ulendo Wautali

PALI mbalame inayake yooneka ngati Nantchengwa yomwe imauluka ulendo wautali kwambiri kuposa mbalame zonse. Mbalameyi imatha kuuluka ulendo wautali makilomita 11,000 m’masiku 8 okha.

Taganizirani izi: Akatswiri ena amanena kuti pali mbalame zina zomwe zimagwiritsa ntchito mphamvu yokoka yadziko zikamauluka, moti zimakhala ngati ubongo wake uli ndi kampasi yomwe imazithandiza kudziwa komwe zikulowera. N’kutheka kuti mbalamezi zimadziwa komwe zikupita pogwiritsa ntchito dzuwa masana komanso nyenyezi usiku. Komanso zikuoneka kuti mbalamezi zimatha kudziwa ngati kukubwera mphepo yomwe imathandiza mbalamezi zikamauluka. Komabe akatswiri sakudziwa bwinobwino chimene chimathandiza kuti mbalamezi ziziuluka mtunda wautali chonchi. Wasayansi wina, dzina lake Bob Gill, ananena kuti: “Ndakhala ndikuphunzira za mbalamezi kwa zaka 20, koma mpaka pano sindizimvetsabe.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti mbalame imeneyi izitha kuuluka mtunda wautali chonchi, kapena pali winawake amene anailenga?