Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndi Bwino Banja Lingotha Basi”

“Ndi Bwino Banja Lingotha Basi”

“Ndi Bwino Banja Lingotha Basi”

Nyumba ikuoneka kuti sikusamalidwa. Kwa zaka zambiri yakhala ikuwombedwa ndi mphepo ndipo ngakhale kuti sinagwe, yasakazika kwambiri. Panopa ikuoneka kuti nthawi ina iliyonse ikhoza kugwa.

ZIMENE tafotokozazi ndi zofanana ndi mmene mabanja ambiri alili masiku ano. Kodi nanunso mukuona kuti banja lanu likukumana ndi mavuto moti likhoza kutha nthawi iliyonse? Ngati ndi choncho, choti mudziwe n’chakuti palibe banja limene silikumana ndi mavuto. Ndipotu Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti anthu ‘olowa m’banja adzakhala ndi nsautso.’—1 Akorinto 7:28.

Posonyeza kuti mfundo imeneyi ndi yoona, gulu lina lochita kafukufuku linanena kuti “ngakhale kuti anthu ambiri amakwatira, banja ndi chinthu chimene chimabweretsa mavuto ambiri pamoyo wa munthu.” Iwo ananenanso kuti: “Banja likamayamba, aliyense amayembekezera kuti azisangalala ndiponso chilichonse chiziyenda bwino, koma kenako amayamba kukumana ndi mavuto aakulu.”

Kodi zinthu zili bwanji m’banja lanu? Kapena banja lanu silikuyenda bwino chifukwa cha zinthu zotsatirazi?

● Kukanganakangana

● Kukalipirana

● Kusakhulupirika

● Kukwiya kwambiri ndiponso kusafuna kulankhulana

Kodi muyenera kutani ngati banja lanu likukumana ndi mavuto ndipo mukuona kuti likhoza kutha nthawi iliyonse? Kodi ndi bwino kungolithetsa?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 3]

“KUTHETSA BANJA SI NKHANI YAIKULU”

M’mayiko ena chiwerengero cha mabanja amene akutha chakwera kwambiri. Mwachitsanzo, kale ku United States mabanja sankatha mwachisawawa. Barbara Dafoe Whitehead analemba m’buku lake kuti, “chiwerengero cha mabanja amene amatha chinawonjezereka mochititsa mantha kwambiri” kuyambira mu 1960. Iye ananenanso kuti: “M’zaka 10 zokha, chiwerengerochi chinawonjezeka kuwirikiza kawiri ndipo chinapitirizabe kukula mpaka kumayambiriro kwa m’ma 1980. Ngakhale kuti kenako chiwerengerochi chinasiya kukwera, chinali chachikulube makamaka m’mayiko ambiri olemera a ku Ulaya. Zimenezi zachititsa kuti m’zaka 30 zokha, anthu ambiri ku America ayambe kuona kuti kuthetsa banja si nkhani yaikulu.”—The Divorce Culture.