Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mayi Wathanzi Amaberekanso Mwana Wathanzi

Mayi Wathanzi Amaberekanso Mwana Wathanzi

Mayi Wathanzi Amaberekanso Mwana Wathanzi

MAYI wanyamula mwana wake amene wangobadwa kumene ndipo mwanayo akuoneka wathanzi ndi wosangalala. Bambo ake akunyadira kwambiri. Koma popeza kuti chaka chilichonse kumabadwa ana ambirimbiri, anthu ena amaona kuti kubadwa kwa mwana si chinthu chapadera. Ndipo amaona kuti munthu aliyense atafuna akhoza kukhala ndi mwana.

Komabe dziwani kuti si amayi wonse amene zimawayendera bwino pobereka. Choncho, makolo anzeru amene akuyembekezera kubereka amachita zonse zotheka kuti mwana wawo adzabadwe bwinobwino. Mwachitsanzo, iwo amafufuziratu zinthu zimene zimachititsa mavuto amene amatha kukhalapo pobereka. Amaonetsetsanso kuti mayi wapakati akulandira chithandizo choyenerera cha kuchipatala. Ndipo iwo amatsatira zinthu zimene zingachepetse mavuto amenewa. Tiyeni tikambirane bwinobwino zimenezi.

Zinthu Zimene Zimayambitsa Mavuto Pobereka

Chinthu chimodzi chimene chimachititsa kuti pakhale mavuto kwa mwana ndiponso mayi ndicho kusalandira chithandizo choyenera panthawi imene mayiyo ali woyembekezera. Dr. Cheung Kam-lau, dokotala wa ana pachipatala cha Prince of Wales ku Hong Kong, anati: “Pamakhala mavuto aakulu ngati mayi salandira chithandizo cha kuchipatala panthawi imene ali woyembekezera.” Iye ananenanso kuti: “Ambiri mwa amayi otere amayembekezera kubereka ana athanzi ndiponso onenepa, koma nthawi zambiri zimenezi sizichitika.”

Magazini ina inanena kuti “amayi ambiri amamwalira pobereka” chifukwa chotaya magazi ambiri, chifukwa choti mwana akukanika kutuluka, chifukwa chothamanga magazi, kapenanso chifukwa cha matenda ena. Magaziniyi inanenanso kuti, mavuto amenewa si odetsa nkhawa chifukwa njira zowathetsera n’zosavuta, ndipo “njira zambiri zamakono . . . sizichita kufuna zipangizo zapamwamba kwambiri.”—Journal of the American Medical Women’s Association.

Si kuti pamachita kufunika chithandizo cha pamwamba kwambiri kuti ana abadwe bwinobwino. Magazini ya UN Chronicle inanena kuti “ana awiri pa ana atatu aliwonse amene amafa angapulumutsidwe ngati mayi komanso mwana atalandira chithandizo cha kuchipatala choperekedwa m’njira yoyenera koma chosachita kufuna zipangizo zapamwamba kwambiri.” Nyuzipepala ina ya ku Philippines inanena kuti, n’zomvetsa chisoni kuti amayi ambiri apakati samadziwa zoyenera kuchita ndiponso samapita kuchipatala kuti akalandire chithandizo.

Njira Yabwino Yothandizira Amayi Ndiponso Ana

Magazini ya UN Chronicle inati: “Mayi wathanzi amaberekanso mwana wathanzi.” Ndipo inanenanso kuti amayi akalandira chithandizo cha kuchipatala chochepa kapena akapanda kulandira chithandizo chilichonse pamene ali woyembekezera, pamene akubereka kapena atangobereka kumene, mwana wawo amalandiranso chithandizo chochepa cha kuchipatala kapena salandira chithandizo n’komwe.

M’mayiko ena n’zovuta kuti mayi woyembekezera apeze chithandizo choyenera cha kuchipatala. Mwina angafunike kuyenda ulendo wautali kuti akafike kuchipatala, kapena sangakwanitse kulipira ndalama zofunika kuchipatala. Komabe, ngati zingatheke, mayi woyembekezera ayenera kuonana ndi akatswiri a zachipatala. Zimenezi n’zofunika kwambiri kwa amayi amene amatsatira mfundo za m’Baibulo, chifukwa Baibulo limanena kuti moyo wa munthu, kuphatikizapo wa mwana wosabadwa, ndi wopatulika.—Eksodo 21:22, 23; * Deuteronomo 22:8.

Kodi zimenezi zikusonyeza kuti mayi woyembekezera ayenera kumakaonana ndi dokotala mlungu uliwonse? Ayi. Ponena za mavuto amene amachitika panthawi yoyembekezera komanso yobereka, Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse “linapeza kuti amayi amene anaonana ndi dokotala kanayi kokha panthawi yonse imene anali ndi pakati,” anabereka bwinobwino “mofanana ndi amayi oyembekezera amene anaonana ndi dokotala maulendo 12 kapena kuposa.”

Zimene Madokotala Angachite

Kuti mayi abereke bwinobwino, madokotala, makamaka amene anaphunzira za uzamba, amatsatira mfundo zotsatirazi:

▪ Amafufuza kuti adziwe matenda amene mayiyo anadwalapo, ndipo amamupima kuti adziwe mavuto amene angakhale nawo pobereka. Kenako amapereka chithandizo choteteza mayiyo komanso mwana wake.

▪ Amatenga magazi ndi mkodzo kuti aone ngati mayiyo akuperewera magazi, ngati magazi a mayi ndi a mwana ndi osiyana, kapenanso ngati mayiyo ali ndi matenda ena. Matendawa ndi monga a shuga, chikuku, matenda opatsirana pogonana, ndi matenda a impso, amene angachititse kuti mayi azithamanga kwambiri magazi.

▪ Ngati zingakhale zoyenerera, mayiyo angabaidwe katemera wa fuluwenza, kafumbata, ndiponso wothandiza kuti magazi a mayi ndi a mwana akhale ogwirizana.

▪ Mayiyo angapatsidwenso mankhwala a mavitamini, makamaka vitamini B.

Ngati madokotala atadziwa mavuto amene mayi woyembekezera angakumane nawo n’kupezeratu njira zomutetezera, moyo wa mayiyo komanso mwana wake sungakhale pangozi.

Kuchepetsa Mavuto Amene Amakhalapo Pobereka

Joy Phumaphi, yemwe anali wachiwiri kwa mlembi woona za umoyo wa mabanja m’Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse, anati: “Nthawi yovuta kwambiri kwa mayi woyembekezera ndi pamene akubereka.” Kodi amayi oyembekezera angathandizidwe bwanji kuti moyo wawo usakhale pangozi panthawi yovuta imeneyi? Pali zinthu zosavuta kuzitsatira zimene amayi oyembekezera angachite ndipo ayenera kuzichita nthawi idakalipo. * Zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka kwa amayi amene salola kuikidwa magazi chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo kapena amene amakana chifukwa choopa matenda.—Machitidwe 15:20, 28, 29.

Amayi amene salola kuikidwa magazi ayenera kuonetsetsa kuti munthu amene akuwathandizayo, kaya ndi dokotala kapena mzamba, ndi wodziwa bwino ntchito yake komanso wakhala akuthandiza anthu popanda kugwiritsa ntchito magazi. Ndiponso amayi oyembekezera ayenera kufufuziratu kuti adziwe ngati ogwira ntchito kuchipatala kapena malo alionse kumene akufuna kukachirira, angathe kuwathandiza popanda kuwaika magazi. * Mungafunse dokotala mafunso awiri otsatirawa: 1. Kodi mudzachita chiyani ngati mayi kapena mwana wataya magazi ambiri kapena ngati patakhala mavuto ena pobereka? 2. Ngati nthawi yobereka itakwana ndipo inuyo mwachoka, kodi anthu ena amene angatithandize adzatsatira zimene tagwirizanazi?

Mayi wanzeru amapita kuchipatala kuti madokotala akamuone n’cholinga choti akamadzachira adzakhale ndi magazi okwanira. Ngati alibe magazi okwanira, madokotala angamulangize mayiyo kuti azidya zakudya zokhala ndi vitamini B komanso ayironi.

Madokotala angaonenso zinthu zina. Mwachitsanzo, angaone ngati mayiyo anali ndi matenda enaake omwe angafunike chisamaliro. Iwo angaonenso ngati mayiyo sakufunika kumagwira ntchito nthawi yaitali ataimirira, ngati akufunika kumagona nthawi yaitali, kapena ngati akufunika kuchita masewera olimbitsa thupi kuti sikelo yake itsike. Angaonenso ngati angafunike kuyesetsa kwambiri kukhala waukhondo, kuphatikizapo kutsuka mano.

Kafukufuku akusonyeza kuti chiseyeye chimayambitsa matenda enaake oopsa amene amachititsa kuti magazi azithamanga, mutu uzipweteka kwambiri, ndiponso kuti thupi lizitupa. * Matenda amenewa amachititsa kuti mwana abadwe masiku asanakwane. Ndipo matendawa ndi amene amachititsa kuti ana ongobadwa kumene komanso amayi ambiri apakati azimwalira, makamaka m’mayiko amene akungotukuka kumene.

Madokotala abwino amaganizira matenda alionse amene mayi woyembekezera angakhale nawo. Ndipo ngati mayiyo akumva kupweteka kwambiri nthawi yochira isanakwane, dokotalayo angaone kuti ndi bwino kuti mayiyo agonekedwe m’chipatala, zomwe zingathandize kupulumutsa moyo wake.

Dr. Quazi Monirul Islam, yemwe ndi mkulu ku dipatimenti yoona za uchembere m’Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse, anati: “Amayi oyembekezera amakhala pa ngozi yoti akhoza kufa pobereka.” Koma atalandira chithandizo choyenerera cha kuchipatala panthawi yomwe ali oyembekezera, pobereka komanso akangobereka, zingathandize kupewa mavuto ambiri, ngakhale imfa imene. Komabe, chofunika kwambiri n’chakuti muziyesetsa kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kukhala ndi thanzi labwino. Ndipo dziwani kuti ngati mukufuna kudzabereka mwana wathanzi, muyenera kuyesetsa kukhala ndi thanzi labwino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mawu a Chiheberi oyambirira ankanena za ngozi imene ingaphetse mwana komanso mayi ake.

^ ndime 21 Ngati ndinu a Mboni za Yehova ndipo mkazi wanu watsala pang’ono kuchira, mungachite bwino kudziwitsa Komiti Yolankhulana ndi Achipatala (HLC) ya kudera kwanu. Anthu a m’komiti imeneyi amayenda m’zipatala kuti athandize madokotala kusamalira odwala a Mboni popanda kugwiritsa ntchito magazi. Komanso anthu a m’komiti imeneyi angathandize kupeza dokotala amene amalemekeza zimene wodwala amakhulupirira komanso amene amadziwa bwino kuthandiza anthu popanda kugwiritsa ntchito magazi.

^ ndime 24 Ngakhale kuti pakufunikirabe kufufuza kuti atsimikizire ngati chiseyeye chimayambitsadi matenda oopsa amenewa, ndi nzeru kuyesetsa kusamalira mano anu.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Malinga ndi lipoti la October 2007, mphindi iliyonse, mayi mmodzi wapakati amafa, ndipo zimenezi zikutanthauza kuti amayi apakati amene amafa pachaka amakwana 536,000.—United Nations Population Fund

[Mawu Otsindika patsamba 28]

“Chaka chilichonse, ana okwana 3.3 miliyoni amabadwa atafa kale ndipo ana oposa 4 miliyoni amene amabadwa ali ndi moyo, amafa pasanathe masiku 28.”—UN Chronicle

[Chithunzi patsamba 29]

 ZOYENERA KUCHITA MAYI AKAKHALA NDI PAKATI

1. Sankhani mwanzeru chipatala, dokotala, kapena mzamba nthawi idakalipo.

2. Muzipita kawirikawiri kuchipatala kukaonana ndi dokotala kapena mzamba wanu, n’cholinga choti mudziwane bwino.

3. Muzisamalira thanzi lanu. Ndipo ngati n’zotheka, muzimwa mankhwala okhala ndi mavitamini oyenera. Koma pewani kumwa mankhwala mwachisawawa, popanda kuuzidwa ndi dokotala. Pewani kumwa mowa. Bungwe lina la ku United States loona za mowa linati: “Ngakhale kuti ana amene amakhudzidwa kwambiri ndi mowa ndi amene amayi awo amamwa kwambiri, sizikudziwika ngati ana amene amayi awo amamwa pang’ono sakhudzidwa.”

4. Ngati mukumva kupweteka kosonyeza kuti mwatsala pang’ono kubereka, (musanakwanitse milungu 37) muyenera kudziwitsa dokotala kapena kupita kuchipatala mwamsanga. Kuthandizidwa mwamsanga kungathandize kuti musabereke nthawi isanakwane komanso kuti mupewe mavuto ena. *

5. Lembani chithandizo chimene mungasankhe kulandira. Mwachitsanzo, ambiri aona kuti ndi bwino kukhala ndi Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala (DPA). Fufuzani kuti mudziwe njira yochitira zimenezi yovomerezeka m’dziko mwanu.

6. Mwana akabadwa, muzionetsetsa kuti mukusamalira thanzi lanu ndi la mwana wanuyo, makamaka ngati wabadwa masiku asanakwane. Ngati mwaona vuto linalake, kaonaneni ndi dokotala wa ana mwamsanga.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 41 Nthawi zambiri ana amene abadwa masiku asanakwane amaikidwa magazi chifukwa chakuti ziwalo zawo zimakhala zisanakhwime moti n’kumapanga zokha maselo ofiira a magazi.