Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

5. Kukwaniritsidwa kwa Ulosi

5. Kukwaniritsidwa kwa Ulosi

Chifukwa Chake Tiyenera Kukhulupirira Baibulo

5. Kukwaniritsidwa kwa Ulosi

Ngati munthu wazanyengo amene amanena zoona nthawi zonse wanena kuti kugwa mvula, kodi mungakayikire n’kunyalanyaza kuyenda ndi ambulera?

M’BAIBULO muli ulosi wosiyanasiyana. * Zimene zalembedwa zokhudza mbiri yakale zimasonyeza kuti ulosi wa m’Baibulo umakwaniritsidwa nthawi zonse.

Ulosi wake ndi wapadera. Nthawi zambiri ulosi wa m’Baibulo umafotokoza mwatsatanetsatane zimene zidzachitike ndipo ulosi wonsewo umakwaniritsidwa. Kawirikawiri ulosi wa m’Baibulo umanena za zinthu zofunika kwambiri ndipo umatchula ngakhale zinthu zimene anthu sakuyembekeza n’komwe.

Chitsanzo chabwino. Mzinda wakale wa Babulo unamangidwa pa malo abwino kwambiri, m’mphepete mwa mtsinje wa Firate, ndipo mzindawo unkadziwika monga “likulu la mayiko a kum’mawa pankhani zandale, chipembedzo, ndi chikhalidwe cha anthu.” Cha mu 732 B.C.E., mneneri Yesaya analemba ulosi wochititsa mantha wonena za kugwa kwa Babulo. Iye anafotokoza zonse zimene zinali kudzachitika. Ananena kuti mtsogoleri wina, dzina lake “Koresi,” ndiye adzagonjetse mzindawo, mtsinje wa Firate womwe unkateteza mzindawo ‘udzauma,’ ndipo ‘zipata zake zidzasiyidwa zosatseka.’ (Yesaya 44:27–45:3) Patapita zaka pafupifupi 200, pa October 5, 539 B.C.E., ulosi umenewu unakwaniritsidwa ndendende. Mgiriki wina wolemba mbiri yakale dzina lake Herodotus (wa m’zaka za m’ma 400 B.C.E.) anatsimikizira nkhaniyi.

Ulosi wodabwitsa. Yesaya analosera chinthu china chodabwitsa chokhudza Babulo kuti: ‘Anthu sadzakhalamonso.’ (Yesaya 13:19, 20) Zinali zosayembekezereka kulosera kuti mzinda waukulu wokhala pamalo otetezeka ngati Babulo, udzawonongedwa n’kukhala bwinja mpaka kalekale. Mungayembekezere kuti mzinda wotere utawonongedwa ungamangidwenso. N’zoona kuti mzinda wa Babulo utagonjetsedwa unakhalapobe kwanthawi ndithu, koma m’kupita kwa nthawi mawu a Yesaya anakwaniritsidwa. Magazini ina inati, masiku ano pamalo pamene panali Babulo “pangotsala fumbi lokhalokha, ndi potentha ndipo sipakhalanso anthu.”—Magazini ya Smithsonian.

Ulosi umenewu ndi wochititsa chidwi kwabasi. Zimene Yesaya analoserazi zingafanane ndi kunena mwatsatanetsatane mmene mzinda wamakono ngati New York kapena London udzawonongedwere patapita zaka 200, ndiponso kunena motsindika kuti mumzindawo simudzakhalanso anthu. Koma chochititsa chidwi kwambiri n’chakuti ulosi wa Yesaya unakwaniritsidwa ndendende. *

M’nkhani zimenezi, tafotokoza zinthu zina zimene zachititsa anthu ambiri kukhulupirira Baibulo. Anthuwa amaliona kuti ndi buku lodalirika limene lingawatsogolere. Bwanji osaphunzira zambiri za Baibulo kuti inunso muone nokha ngati mungalikhulupirire kapena ayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Zimene azanyengo amanena nthawi zina sizichitika. Koma ulosi wa m’Baibulo sulephera chifukwa umachokera kwa Mulungu, amene angasinthe zinthu kuti zichitike mmene iye akufunira.

^ ndime 8 Kuti muone zitsanzo zina za ulosi wa m’Baibulo ndiponso umboni wa m’mbiri yakale woti unakwaniritsidwa, onani masamba 117 mpaka 133 a buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 9]

Baibulo linalosera molondola kuti mtsogoleri wina, dzina lake Koresi, ndiye adzagonjetse mzinda wamphamvu wa Babulo