Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

INDONESIA

Sitinalole Kusiya Zimene Timakhulupirira

Daniel Lokollo

Sitinalole Kusiya Zimene Timakhulupirira
  • CHAKA CHOBADWA 1965

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1986

  • MBIRI YAKE Mpainiya wapadera amene anakhalabe wokhulupirika pa nthawi imene ankazunzidwa.

PA 14 April, 1989, akuluakulu a boma anandimanga pamodzi ndi anthu ena atatu. Pa nthawiyi ndinkachititsa msonkhano wa mpingo m’tauni ya Maumere pachilumba cha Flores.

Oyang’anira ndende ya m’derali anatikakamiza kuti tizichitira sailuti mbendera. Titakana, anatimenya n’kutikhazika panja kwa masiku 5, dzuwa likutentha kwambiri. Ndipo usiku, tinkazizidwa kwambiri chifukwa tinkagona pasimenti mundende zomwe zinali zazing’ono kwambiri komanso zauve. Nthawi zonse tinkakhala otopa komanso tinkamva kupweteka kwambiri chifukwa cha mabala. Woyang’anira ndendeyi ankatikakamiza kuti tingosiya zimene timakhulupirira koma tinamuuza kuti: “Tilolera kufa koma singachitire sailuti mbendera.” Ifenso tinaona kuti ndi mwayi wathu ‘kuvutika chifukwa cha chilungamo’ mofanana ndi Akhristu akale.—1 Pet. 3:14.