Pitani ku nkhani yake

Malangizo a Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Malangizo a Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Zimene Zili Papepala la Malangizoli

1. Malangizo amene ali mu kabuku kano, azithandiza aliyense amene ali ndi mbali pa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Anthu amenewa, akuyenera kuonanso malangizo amene ali mu kabuku ka Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu limodzi ndi malangizo amene ali m’kabuku kano asanachite mbali imene apatsidwa ku mpingo. Ofalitsa onse akuyenera kulimbikitsidwa kuti alembetse n’cholinga choti azipatsidwa nkhani za ophunzira. Anthu enanso amene amasonkhana ndi mpingo nthawi zonse ndipo amatsatira mfundo zimene Baibulo limaphunzitsa komanso mfundo zachikhristu pa moyo wawo, angalembetse kuti azipatsidwa nkhani za ophunzirazi. Oyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu akuyenera kukambirana zimene zimafunikira kuti munthu alembedwe mu sukulu ndi aliyense amene si ofalitsa koma ali ndi chidwi chofuna kulembetsa mu sukulu ya utumiki, azimuthandiza kuona ngati ali woyenera kulembetsa nawo. Zimenezi zikuyenera kuchitika ali limodzi ndi munthu amene amachita naye phunziro la Baibulo ( kapena makolo ake amene ndi a mboni). Zinthu zimene munthu amafunikira kuti ayambe kutenga nawo mbali mu sukulu ya utumiki, ndi zofanana ndi zimene zimafunikira kuti akhale wofalitsa wosabatizidwa. —od Mutu 8 ndime 8.

 MAWU OYAMBA

2. 1 Miniti. Mlungu uliwonse, pambuyo pa nyimbo yoyamba komanso pemphero, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azifotokoza mwachidule zimene tiphunzire. Tcheyamaniyo azitsindika kwambiri mfundo zimene abale ndi alongo angapindule nazo kwambiri.

  CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 3Nkhani: 10 minitsi. Pa kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu pazikhala mutu komanso mfundo zikuluzikulu ziwiri kapena zitatu. Nkhaniyi iyenera kuperekedwa kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera. Tikamayamba buku latsopano la m’Baibulo, tizionera vidiyo. Ndiyeno wokamba nkhaniyo azisonyeza kugwirizana pakati pa vidiyoyo ndi mutu umene uli mu kabuku. Koma ayeneranso kuonetsetsa kuti wafotokoza mfundo zimene zili m’kabukuko. Komanso ngati nthawi ilipo, ayenera kufotokozera zithunzi zimene zaikidwa zomwe zimakonzedwa kuti zithandize kumveketsa mfundo za m’nkhaniyo. Akhozanso kuwonjezera malifalensi ena amene akuthandiza kumveketsa bwino mfundo za m’nkhani yake.

 4. Mfundo Zothandiza: 10 minitsi. Iyi ndi nkhani ya mafunso ndi mayankho yopanda mawu oyamba ndiponso omaliza. Nkhaniyi izikambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera. Iye ayenera kufunsa mafunso onse awiri. Komanso, akhoza kusankha kuwerenga mavesi onse amene aikidwa kapena ayi. Anthu amene atchulidwa kuti ayankhe ayenera kufotokoza ndemanga zawo kwa nthawi yosapitirira masekondi 30.

  5. Kuwerenga Baibulo: 4 Minitsi. Nkhaniyi iperekedwe kwa wophunzira wamwamuna. Ayenera kungowerenga mavesi amene wauzidwa popanda kunena mawu oyamba kapena omaliza. Tcheyamani ayenera kuthandiza munthuyo kuti amvetse zimene akuwerenga, awerenge molondola komanso mosadodoma, azisintha mawu, kupuma moyenera ndiponso kulankhula mwachibadwa. Popeza kuti mavesi ena amene abale azipatsidwa kuti awerenge azikhala ambiri ndipo ena azikhala ochepa, woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu ayenera kuganizira luso la wophunzira akamagawa nkhani zimenezi.

 KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

6. 15 Minitsi. Chigawo chimenechi cha msonkhano chakonzedwa kuti chizithandiza aliyense kuyeserera zimene angachite mu utumiki komanso kuwonjezera luso lolalikira ndi kuphunzitsa. Ngati kuli kotheka, akulu akuyenera kupatsidwa mbali zina za ophunzira. Wophunzira aliyense akuyenera kugwirirapo ntchito pa phunziro limene wapatsidwa kuti agwiritse ntchito kuchokera mu kabuku ka Kuphunzitsa kapena kabuku ka Muzikonda Anthu. Timabukuti timasonyezedwa mikutira mawu mu Kabuku ka Utumiki komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Nthawi zina pazikonzedwa dongosolo lakuti anthu akambirane mfundo zina. Mbali yokambiranayi, ikuyenera kuperekedwa kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera.—Onani  ndime 15 pa nkhani ya m’mene nkhani yokambirana ikuyenera kuchititsidwira.

 7. Ulendo Woyamba: Nkhaniyi iperekedwe kwa munthu wamwamuna kapena wa mkazi. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamkazi, mwininyumba akhalenso munthu wamkazi ndipo ngati yaperekedwa kwa munthu wamwamuna, mwininyumba akhalenso munthu wamwamuna kapena munthu wa m’banja lake. Wophunzira komanso womuthandizira wake angasankhe kukhala pansi kapena kuimilira akamachita chitsanzochi. Kuti mudziwe zambiri zokhudza cholinga komanso mtundu wa ulaliki womwe mukufuna kuchita pa chitsanzo chanu,  onani ndime 12 ndi  13.

 8. Ulendo Wobwereza: Nkhaniyi iperekedwe kwa munthu wamwamuna kapena wa mkazi. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamkazi, mwininyumba akhalenso munthu wamkazi ndipo ngati yaperekedwa kwa munthu wamwamuna, mwininyumba akhalenso munthu wamwamuna. (km 5/97 p.2) Wophunzira komanso womuthandizira wake angasankhe kukhala pansi kapena kuimilira akamachita chitsanzochi. Wophunzira akuyenera kuonetsa zimene anganene pofuna kuyambitsa nkhani yomwe anakambirana kale ndi mwini nyumba pa ulendo woyamba. Kuti mudziwe zambiri zokhudza cholinga komanso mtundu wa ulaliki womwe mukufuna kuchita pa chitsanzo chanu,  onani ndime 12 ndi  13.

 9. Kuphunzitsa Anthu: Nkhaniyi iperekedwe kwa munthu wamwamuna kapena wa mkazi. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamkazi, mwininyumba akhalenso munthu wamkazi ndipo ngati yaperekedwa kwa munthu wamwamuna, mwininyumba akhalenso munthu wamwamuna. (km 5/97 p.2) Wophunzira komanso womuthandizira wake angasankhe kukhala pansi kapena kuimilira akamachita chitsanzochi. Nkhaniyi izisonyeza phunziro la Baibulo lomwe layamba kale kuchitika. Palibe chifukwa chokhala ndi mawu oyamba kapena omaliza, pokhapokha ngati mutu wa phunziro limene wophunzirayo wapatsidwa ukunena zimenezo. Sizofunika kuwerenga ndime zonse zimene mwapatsidwa, ngakhale kuti mungasankhe kuwerenga.

 10. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira: Ngati ikambidwe ngati nkhani, mbali imeneyi ikuyenera kuperekedwa kwa ophunzira wamwamuna. Koma ngati ikhale monga chitsanzo, ingaperekedwe kwa ophunzira kwa mkazi kapena wamwamuna. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamkazi, mwininyumba akhalenso munthu wamkazi ndipo ngati yaperekedwa kwa munthu wamwamuna, mwininyumba akhalenso munthu wamwamuna. Wophunzira akuyenera kupereka yankho lomveka bwino komanso mochenjera akamayankha funso la mutu wa nkhani yake potengera malifalensi amene anapatsidwa. Wophunzira angasankhe kutchula lifalensi imene anagwiritsa ntchito pofufuza kapena ayi pa nthawi imene akukamba nkhani yake.

 11. Nkhani: Mbali imeneyi ikuyenera kuperekedwa kwa munthu wamwamuna ndipo izikambidwa monga nkhani ku mpingo. Ngati nkhaniyo yachokera pa Zakumapeto A m’kabuku ka Muzikonda Anthu, wophunzirayo akuyenera kufotokoza m’mene mavesiyo angagwiritsidwire ntchito muutumiki. Mwachitsanzo, angafotokoze nthawi imene lembalo lingagwiritsidwe ntchito, tanthauzo lake komanso m’mene tingaligwiritsire ntchito pokambirana ndi munthu. Ngati nkhani yake ikuchokera pa limodzi mwa phunziro lomwe lili mu kabuku ka Muzikonda Anthu, chidwi chake chizikhala kwambiri pa m’mene tingagwiritsire ntchito mfundozo mu utumiki. Angafotokoze chitsanzo chimene chili pa mfundo yoyambirira pa phunzirolo kapena angafotokoze malemba ena owonjezera pa phunzirolo amene ali othandiza.

   12. Cholinga: Mfundo zimene zili pa ndime ino komanso zotsatirazi, zikufotokoza kwambiri m’mene tingachitire pa mbali ya “Ulendo Woyamba” komanso “Ulendo Obwereza”. Cholinga cha ophunzira chikuyenera kukhala pa kufotokoza mfundo zachidule za choonadi cha M’Baibulo kwa munthu amene akuyankhula naye komanso kuonetsetsa kuti apanga maziko a ulendo wobwereza. Wophunzira akuyenera kusankha nkhani yoti akambirane yomwe ndi yogwira mtima m’deralo komanso yosatenga nthawi yambiri. Angasankhe ngati akufunika kugawira mabuku, kuonetsa vidiyo kapena ayi. M’malo mongoloweza zoyenera kunena n’kumayankhula, ophunzira akuyenera kuwonjezera luso lawo lokambirana ndi anthu pokamba nkhani zawo mwaumoyo komanso kumasonyeza chidwi kwa omvetsera.

   13. Mtundu wa Ulaliki: Ophunzira akuyenera kugwiritsa ntchito mtundu wa ulaliki umene apatsidwa mogwirizana ndi m’mene zinthu zilili m’dera lanulo. Mwachitsanzo:

  1.  (1) Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba: Mtundu wa ulaliki umenewu umaphatikizapo kulalikira khomo ndi khomo kukumana ndi anthu, kuimba ma foni kapenanso kulemba makalata. Zimaphatikizanso kupanga maulendo obwereza kwa anthu amene tinawalalikirawa.

  2.  (2) Ulaliki wa Mwamwayi: Mtundu wa ulaliki umenewu umaphatikizapo kuyamba kulalikira kwa anthu kuchokera pa nkhani zina zimene tikucheza nawo ndipo kenako timayamba kuwafotokozera mfundo za choonadi. Zingaphatikizepo kufotokoza mfundo za M’Baibulo ndi anthu amene timagwira nawo ntchito, amene timaphunzira nawo sukulu, amene tayandikana nawo nyumba, takwera nawo limodzi galimoto kapenanso kulikonse komwe tingakumane nawo tikamachita zinthu zathu za tsiku ndi tsiku.

  3.  (3) Ulaliki wa Pamalo Opezeka Anthu Ambiri: Mtundu wa ulaliki umenewu ukuphatikizapo kulalikira ndi timashelefu, kulalikira anthu pamalo anthu a malonda, ulaliki wa munsewu, kulalikira kumapaki, koimika magalimoto kapena malo alionse opezeka anthu ambiri.

 14. Kugwiritsa Ntchito Mavidiyo ndi Mabuku: Kutengera ndi m’mene zinthu zilili, wophunzira angasankhe ngati angakonde kuonetsa vidiyo kapena kugawira buku. Ngati nkhani ya wophunzira ikufunika kuonetsa vidiyo kapena iye wasankha kugwiritsa ntchito vidiyo, akuyenera kuifotokoza ndipo kenako akambirane mfundo za muvidiyoyo koma sakuyenera kuisewera.

  MOYO WATHU WACHIKHRISTU

15. Nyimbo ikatha, 15 minitsi yotsatira ya chigawochi izikhala ndi nkhani imodzi kapena ziwiri zothandiza anthu kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu pamoyo wawo. Nkhanizi zingaperekedwe kwa akulu kapena atumiki othandiza oyenerera. Koma ngati ndi zofunika pampingo ziyenera kukambidwa ndi akulu okha. Ngati nkhaniyi ili yokambirana, wokamba nkhaniyi angafunse mafunso pa mbali yonse ya nkhaniyi kuphatikizanso mfundo zina zomwe wapatsidwa. Akuyenera kukhala ndi mawu oyamba achidule n’cholinga chopereka nthawi yokwanira yokambirana mfundo zonse komanso kupereka mwayi kwa osonkhana kupereka ndemanga. Ngati nkhaniyi ikukhudza kufunsa ena mafunso, ndi zoyenera kuti ofunsidwawo azikaperekera ndemanga zawo ali ku pulatifomu m’malo moyankha atakhala pamalo awo.

  16. Phunziro la Baibulo la Mpingo: 30 minitsi. Iperekedwe kwa mkulu woyenerera. (M’mipingo yomwe akulu ndi ochepa kwambiri, atumiki othandiza oyenerera angapatsidwe mbali imeneyi ngati pakufunika kutero.) Bungwe la akulu likuyenera kuona luso lophunzitsa la mkulu aliyense kuti lisankhe akulu amene ali oyenerera kuchititsa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Akulu amene angasankhidwewo akuyenera kuchititsa phunziroli mogwira mtima, kuthandiza omvera kuti afotokoze mfundo zothandizadi pa malemba oyenerera, kuthandiza aliyense kuti aone mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’phunziroli pa moyo wake, ndipo sayenera kudya nthawi. Abale amene asankhidwa kuti azichititsa phunziroli akuyenera kuwerenga ndi kutsatira mfundo zimene gulu lafalitsa zokhudza mmene tingachititsire nkhani ya mafunso ndi mayankho (w23.04 p.24, kabokosi). Ngati mwamaliza kukambirana mfundo zonse za nkhani ya mlunguwo, palibe chifukwa chotalikitsira phunzirolo pongofuna kumaliza nthawi imene yatsala. Ngati zili zotheka, mlungu uliwonse Phunziro la Baibulo la mpingo lizichititsidwa ndi m’bale wina ndipo m’bale winanso aziwerenga ndime, osati m’bale amene anawerenga mlungu wapita. Ngati tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu wanena kuti phunziroli lichitike mwachidule chifukwa cha nthawi, m’bale amene akuchititsa phunziroli azisankha yekha mmene angalichititsire mwachidule. Iye akhoza kusankha kuti ndime zina zisawerengedwe koma angofunsa mafunso.

  MAWU OMALIZA

17. 3 minitsi. Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azibwereza mwachidule mfundo zothandiza zimene taphunzira pa msonkhanowo. Azitchulanso mwachidule zimene tidzaphunzire mlungu wotsatira. Ngati nthawi ilipo angatchule mayina a anthu amene apatsidwa nkhani mlungu wotsatira. Tcheyamani akhozanso kupereka zilengezo zofunika kapena kuwerenga makalata pa nthawi imeneyi. Zilengezo za nthawi zonse, monga zokhudza kulowa mu utumiki wa kumunda kapena kuyeretsa Nyumba ya Ufumu sizikuyenera kulengezedwa koma zizingoikidwa pabolodi la mpingo. Ngati zilengezo n’zambiri kapena kalata ndi yaitali ayenera kupeza nthawi kapena kupempha abale a nkhani pa gawo lakuti Moyo Wathu Wachikhristu, kuti azifupikitse. (Onani  ndime 16 ndi  19.) Msonkhanowu uzitha ndi nyimbo ndi pemphero.

  KUYAMIKIRA NDIPONSO KUPEREKA MALANGIZO

18. Wophunzira aliyense akamaliza nkhani yake, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azimuyamikira ndiponso kumupatsa malangizo kwa nthawi yosapitirira 1 miniti, ndipo malangizowo azichokera pa phunziro limene anapatsidwa. Tcheyamani akatchula nkhani imene wophunzira akukamba, asatchulenso phunziro limene wapatsidwa. Koma akamaliza, tcheyamaniyo ayenera kumuyamikira ndipo angatchule phunziro limene anapatsidwa, kufotokoza mbali imene wachita bwino kapena zimene ayenera kusintha ulendo wotsatira. Tcheyamani angasankhenso kuyamikira kapena kupereka malangizo pa mbali zina zokhudza mmene wophunzirayo wakambira nkhani yake ngati akuona kuti zingathandize wophunzirayo kapena omvera. Tcheyamani angaperekenso malangizo othandiza kwa wophunzira misonkhano ikatha kapena tsiku lina ndipo malangizowo ayenera kuchokera m’kabuku ka Muzikonda Anthu komanso m’kabuku la Kuphunzitsa kapena buku la Sukulu ya Utumiki. Malangizowo angachokere pa phunziro limene wophunzirayo anapatsidwa kapena pa phunziro lina.—Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya udindo wa tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndiponso udindo wa mlangizi wothandiza, onani  ndime 19,  24 ndi  25.

     KUSUNGA NTHAWI

19. Mbali iliyonse komanso ndemanga za tcheyamani zisapitirire nthawi yake. Ngakhale kuti Kabuku ka Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu kamaikiratu nthawi ya mbali iliyonse, ngati mwamaliza kufotokoza mfundo zonse za mbali yanu simukuyenera kuwonjezera zinthu zina kuti mukwaniritse nthawi yonse yomwe munapatsidwa. Ngati mbali zina za pamisonkhano zapitilira nthawi yake, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu kapena Mlangizi wothandiza akuyenera kupereka malangizo kwa amene wapitilira nthawi yakeyo pambuyo pa misonkhano. (Onani  ndime 24 ndi  25.) Msonkhano wonse kuphatikiza nyimbo ndi pemphero zisapitirire ola limodzi ndi 45 minitsi.

 WOYANG’ANIRA DERA AKAMACHEZERA MPINGO

20. Woyang’anira dera akamachezera mpingo, mapulogalamu aziyenda mmene tasonyezera mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Koma nkhani yautumiki imene woyang’anira dera amakamba kwa 30 minitsi izilowa m’malo mwa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Nkhani ya utumikiyo isanayambe, tcheyamani ayenera kubwereza zimene taphunzira, kutchula pang’ono zimene tiphunzire mlungu wotsatira, kulengeza zinthu zofunika, kuwerenga makalata ngati alipo kenako kuitana woyang’anira derayo kuti adzakambe nkhani yake. Woyang’anira derayo akamaliza nkhani yake adzauza anthu kuti aimbe nyimbo yomaliza imene iye wasankha. Angathe kupempha m’bale wina kuti adzatseke ndi pemphero. Kalasi B ya m’chinenero cha mpingowo sikuyenera kuchitika pa mlungu umene woyang’anira dera akuchezera mpingo. Koma kagulu kayenera kuchitabe misonkhano yake ngakhale kuti woyang’anira dera akuchezera mpingo umene umathandiza kaguluko. Koma pa nthawi imene woyang’anira dera akukamba nkhani yautumiki, kaguluko kakuyenera kumvetsera nkhaniyo.

 WIKI YA MSONKHANO WADERA KAPENA WACHIGAWO

21. Ngati muli ndi msonkhano wadera kapena wachigawo, misonkhano yampingo ya mlunguwo siyenera kuchitika. Mpingo ukuyenera kukumbutsidwa kuti ukuyenera kuphunzira mfundo za pa misonkhano ya mpingoyo pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja kapena pophunzira pawokha.

 WIKI YA CHIKUMBUTSO

22. Misonkhano ya mpingo ya mkati mwa wiki sikuyenera kuchitika ngati tsiku la Chikumbutso lilinso mkati mwa wiki.

 WOYANG’ANIRA MSONKHANO WA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU

23. Bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu mmodzi kuti akhale woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Iye azionetsetsa kuti msonkhanowu ukuchitika mwadongosolo komanso motsatira malangizo amene tafotokozawa. Ayeneranso kuchita zinthu mogwirizana ndi mlangizi wothandiza. Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu kakangofika, iye ndi amene azigawa nkhani zonse za misonkhano ya mkati mwa mlungu kwa miyezi iwiri. Zimenezi zikuphatikizapo nkhani za ophunizira, nkhani zimene siziperekedwa kwa ophunzira komanso amene adzakhale ma tcheyamani kuchokera pa abale amene bungwe la akulu linasankha.(Onani  ndime 3-16 ndi  24.) Akamapereka nkhani kwa ophunzira, akuyenera kuganizira zinthu monga: zaka za wophunzirayo, ngati ali wodziwa zambiri kapena ayi komanso ufulu wake wakulankhula pa nkhani imene akukambayo. Akuyeneranso kugwiritsa ntchito mfundo zomwezo akamapereka mbali zina za misonkhanoyi. Aliyense amene wapatsidwa nkhani za ophunzira ayenera kudziwitsidwa kutatsala milungu yosachepera itatu kuti akambe nkhaniyo, pogwiritsa ntchito fomu ya Nkhani ya mu Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (S-89). M’bale amene amayang’anira msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ayenera kuonesetsa kuti ndandanda ya misonkhano yonse yaikidwa pa bolodi la mpingo. Bungwe la akulu lingasankhe mkulu wina kapena mtumiki wothandiza kuti azimuthandiza. Komabe akulu okha ndi amene ayenera kugawa nkhani zimene siziperekedwa kwa ophunzira.

    TCHEYAMANI WA MSONKHANO WA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU

24. Mlungu uliwonse, mkulu azipemphedwa kukhala tcheyamani wa msonkhanowu. (Mipingo yomwe ili ndi akulu ochepa kwambiri, atumiki othandiza oyenerera angapemphedwe kukhala tcheyamani, ngati pakufunika kutero.) Tcheyamani azikamba mawu oyamba ndi omaliza. Aziitananso okamba nkhani zosiyanasiyana za msonkhanowu ndipo ngati akulu ndi ochepa, akhoza kumakambanso nkhani zina. Tcheyamani azilankhula mwachidule kwambiri nkhani iliyonse ikatha komanso akamaitana wokamba nkhani yotsatira. Bungwe la akulu liyenera kusankha akulu oyenerera kuti azikhala matcheyamani ndipo azisinthanasinthana. Malinga ndi mmene zilili pa mpingopo, mwina woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu angamakhale tcheyamani mobwerezabwereza kusiyana ndi akulu ena. Mkulu amene anavomerezedwa kuti azichititsa Phunziro la Baibulo la Mpingo ndiye kuti ndi woyeneranso kukhala tcheyamani wa msonkhanowu. Mkulu amene wasankhidwa kukhala tcheyamani ayenera kupereka malangizo achikondi komanso kuyamikira abale ndi alongo amene akamba nkhani za ophunzira. Tcheyamani ayenera kuonetsetsanso kuti misonkhano ikutha pa nthawi yake. (Onani  ndime 17 ndi  19.) Ngati tcheyamani angakonde komanso ngati kupulatifomu kuli malo okwanira, iye akhoza kuima pa maikofoni ena pambali kuti azilankhulirapo, amene akukamba nkhani yotsatira atafika kale pamaikofoni ake. Akhoza kusankhanso zokhaliratu kupulatifomuko pampando ataikanso tebulo lake kuti aziitana amene akukamba nkhani za ophunzira ndiponso kuwapatsa malangizo ali kupulatifomu komweko. Izi zingathandize kuti nthawi isawonongeke.

   MLANGIZI WOTHANDIZA

25. Ngati n’zotheka, sankhani mkulu amene amakamba bwino nkhani kuti akhale mlangizi wothandiza. Mlangiziyu azipereka malangizo kwa akulu ndi atumiki othandiza amene akamba nkhani zosiyanasiyana pamisonkhano yonse yampingo kaya ndi Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, nkhani ya onse, Phunziro la Nsanja ya Olonda kapena Phunziro la Baibulo la Mpingo. (Onani  ndime 19.) Ngati mumpingomo muli akulu ambiri amene amakamba bwino nkhani, mungamasinthe mlangizi wothandiza chaka chilichonse. N’zosafunika kuti mlangizi wothandiza azipereka malangizo pamapeto a nkhani iliyonse.

 MAKALASI ENA

26. Mipingo ingakhale ndi makalasi angapo mogwirizana ndi kuchuluka kwa ophunzira. Kalasi iliyonse ikhale ndi woyang’anira woyenerera ndipo ngati n’kotheka akhale mkulu. Mtumiki wothandiza woyenerera angagwiritsidwenso ntchito kukalasi B ngati zili zoyenera kutero. Bungwe la akulu liyenera kusankha m’bale kapena abale amene angakhale pa udindo umenewu, komanso ngati zili zofunika kuti abalewo azisinthanasinthana. Mlangiziyo ayenera kutsatira malangizo amene ali mu  ndime 18. Anthu ayenera kupemphedwa kuti apite kukalasi B pambuyo pa mbali yakuti Mfundo Zothandiza m’chigawo cha Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu. Iwo ayenera kubwerera kukakhala limodzi ndi mpingo wonse pambuyo pa nkhani yomaliza ya wophunzira.

 MAVIDIYO

27. Pamsonkhanowu tizionera mavidiyo amene asankhidwa. Mavidiyo amene tizionera pamsonkhanowu azipezeka pa pulogalamu ya JW Library˙ ndipo azitheka kuwatsegula pa zipangizo zosiyanasiyana.

© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

S-38-CN 11/23