Kukhulupirira Mulungu

Chikhulupiriro n’champhamvu kwambiri ndipo chimathandiza munthu kukhala ndi mtendere wam’maganizo panopa komanso chiyembekezo chodalirika cham’tsogolo. Ngati simunakhulupirirepo Mulungu, munasiya kumukhulupirira kapenanso mukufuna kulimbitsa chikhulupiriro chanu, Baibulo lingakuthandizeni.