’Lalikirani Uthenga Wabwino’

Msonkhano wa Mboni za Yehova wa 2024

Simudzalipira kuti mulowe komanso sikudzakhala kuyendetsa mbale ya zopereka

Zomwe Zili Pamsonkhanowu

Lachisanu: Mudzaona umboni wosonyeza kuti nkhani zokhudza moyo wa Yesu zomwe zili m’mabuku a Uthenga Wabwino ndi zolondola. Mudzaonanso mmene nkhani zimenezi zingatithandizire masiku ano.

Loweruka: Kodi ndi maulosi ati amene ananenedweratu okhudza kubadwa kwa Yesu komanso moyo wake ali mwana, nanga kodi maulosi amenewa anakwaniritsidwadi?

Lamlungu: Mu nkhani ya mutu wakuti “N’chifukwa Chiyani Sitimaopa Uthenga Woipa?” Mudzaona chimene chikuchititsa anthu mamiliyoni ambiri masiku ano kuona kuti ndi otetezeka komanso kukhulupirira kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo ngakhale kuti panopa zikungoipiraipirabe.

Vidiyo

Moyo wa Yesu Komanso Utumiki Wake: Vidiyo Yoyamba

Kuwala Kwenikweni kwa Dziko

Kubadwa kwa Yesu mozizwitsa chinali chinthu choyamba pa zinthu zambiri zochititsa chidwi zimene zinachitika iye ali mwana. Mfumu ina yankhanza inkafuna kumupha, choncho makolo ake anapita naye ku Iguputo. Pa nthawi ina, anadabwitsa aphunzitsi akuluakulu a mu nthawi yake. Mudzaona zimenezi ndi zinanso Lachisanu ndi Loweruka mu vidiyo ya mbali ziwiri.

Onerani mavidiyo otsatirawa okhudza msonkhano wachaka chino

Kodi Pamisonkhano Yathu Ikuluikulu Pamachitika Zotani?

Onani zomwe zimachitika pamisonkhano ya Mboni za Yehova.

Msonkhano wa Mboni za Yehova wa 2024 Wakuti: ‘Lalikirani Uthenga Wabwino’

Onani zina zomwe zili pamsonkhano wachaka chino.

Zimene Zili Muvidiyo Yakuti: Moyo wa Yesu Komanso Utumiki Wake

Ambiri amadziwa zokhudza kubadwa kwa Yesu komwe kunali kozizwitsa. Koma kodi chinachitika n’chiyani Yesu asanabadwe komanso pambuyo poti wabadwa?